Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga

Pali Surah zina zomwe zalamuridwa kuti ziziwerengedwa nthawi yodziwika usiku ndi usana kapena masiku ena a sabata. Ndi mustahab kwa munthu kuwerenga ma surah amenewa mu nthawi yake yoikidwa.

1. Werengani Surah Kaafiroon musanagone.

Olemekezeka Jabalah bun Haarithah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adati: “Ukamakagona, werenga Surah Kaafiruun mpaka kumapeto kwa surayi, pakuti ndithu, kuwerenga surayi ndi njira yopulumukira ku shirk.”[1]

2. Werengani ma Quls atatu (Surah Ikhlaas, Surah Falaq ndi Surah Naas) katatu m’mawa ndi madzulo aliwonse.

Abdullah bin Khubaib (Radhwiyallahu anhu) adati: Nthawi ina, muusiku wamdima komanso wamvula, tidanyamuka kupita kukamufunafuna Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) kuti atitsogolere swalah. Kenako ndinakumana ndi Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) ndipo anandiuza kuti, “Werenga.” Koma (posadziwa zoti ndinene), sindinawerenge kalikonse. Anandiuzanso kachiwiri, “Werenga.” Koma (posadziwa zoti ndinene), sindinawerenge kalikonse. Anandiuza kachitatu kuti, “Werenga.” Kenako ndinafunsa kuti, “Kodi ndiwerenge chiyani, O Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam)?” Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anayankha kuti: “Werenga Surah Ikhlaas ndi Mu’awwazatain (Surah Falaq ndi Surah Naas) m’mawa ndi madzulo katatu, zidzakukwanirani kukhala mchitetezo ku zoipa zonse.”[2]

3. Werengani Surah Waaqi’ah usiku.

Olemekezeka Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu anhuma) adasimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: Amene amawerenga Surah Waaqi’ah usiku uliwonse, umphawi siudzamupeza.” Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu anhuma) akunenanso kuti: “Ine ndawalangiza ana anga aakazi kuti aziwerenga surah iyi usiku uliwonse.”[3]

Pamene Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu anhuma) atatsala pang’ono kumwalira ali chigonere pa kama wake Uthmaan (Radhwiyallahu anhu), yemwe anali Khalifah pa nthawiyo, anabwera kudzamuona. Pa ulendowo, Uthmaan (Radhwiyallahu anhu) anamufunsa kuti, “Kodi ine ndingalamure kuti mupatsidwe ndalama?” Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu anhuma) anayankha kuti, “Sindikufunikira zimenezo.” Uthmaan (Radhwiyallahu anhu) anayankha: “Chilolezo chidzakhala cha ana anu aakazi (mukadzamwalira).” Pazimenezi Abdullah bin Mas’uud adayankha: “Kodi ukuopa kuti ana anga aakazi adzasauka? (Musakhale ndi mantha amenewa) Ine ndinawalangiza ana anga aakazi kuti aziwerenga Surah Waaqi’ah usiku uliwonse. Ndithu, ine ndinamumva Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) akunena kuti: ‘Munthu amene amawerenga Surah Waaqi’ah usiku uliwonse, umphawi siudzamupeza.[4]


[1] المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 2195، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله في مجمع الزوائد، الرقم: 17033: رواه الطبراني ورجاله وثقوا

[2] سنن الترمذي، الرقم: 3575، وقال: هذا حديث حسن صحيح غريب من هذا الوجه

[3] عمل اليوم والليلة لإبن السني، الرقم: 680 ، شعب الإيمان للبيهقي، الرقم: 2269، وقال المباركفوري في مرعاة المفاتيح 7/255:  وحديث ابن مسعود أخرجه أيضاً ابن السني ونسبه السيوطي في الإتقان للبيهقي والحارث ابن أبي أسامة وأبي عبيد وإسناد ابن السني حسن

[4] أسد الغابة: 3/77

Check Also

Nthawi Zomwe Ma Dua Amayankhidwa

Nthawi ya Azaan ndi Pamene Magulu Awiri Akumana Pankhondo Olemekezeka Sahl bin Sa’d (Radhwiyallahu anhu) …