Chisilam ndi njira yokhayo imene imamutsogolera munthu ku chikondi cha Allah Ta’ala komanso chimamutsogolera Jannah. kudzera mukutsatira machitidwe a chisilamu, Munthu adzapeza chisangalaro cha Allah Ta’ala komanso adzapedza chipambano chosatha.
Muntchito zokakamizidwa zonse mchisilamu, swalah ndi imene ili pamwamba kwambiri pachikakamizo, Mtumiki wa Allah (Swallallah alayhi wasallam) adati; “Swalah ndi kiyi ya ku Jannah.”
Mu Hadith ina, Mtumiki wa Mulungu (Swallallah alayhi wasallam adati, “Swalaah ndikuwala (kuwala mwauzimu).””
Choncho ngati wina akufuna kuwalitsa umoyo wake, akuyenera kuwalitsa umoyo wake ndi swalah.
Pakadali pano, Maiko ochuluka kuzungulira dziko lapansi akukhudzidwa ndi mavuto adzachuma. Ndimavuto azachumawa, Ndondomeko komanso njira zosiyanasiyana zikutsatiridwa ndi cholinga chobwezeretsa ndikukweza chuma chadziko.
Komabe Quraan Majiid ndi Ma Hadith a Mtumiki (Swallallah alayhi wasallam), Allah Ta’ala ndi Mtumiki zalumikizitsa madalitso a mariziq ndizofunikira pa umoyo kudzera mu swalah.
Mu Quraan Majiid, Allah akuti:
وَأْمُرْ أَهْلَكَ بِالصَّلَاةِ وَاصْطَبِرْ عَلَيْهَا ۖ لَا نَسْأَلُكَ رِزْقًا ۖ نَّحْنُ نَرْزُقُكَ ۗ وَالْعَاقِبَةُ لِلتَّقْوَىٰ ﴿١٣٢﴾
Lamulira banja lako kupemphera swalah ndipo limbikira kutero. Sitimakupemphani mariziq, Ife ndi amene timapereka mariziq kwa inu .
Olemekezeka Abdullah bin Salaam (Radhwiyallah anhu) akusimba kuti; pamene akubanja a Mtumiki (Swallallah alayhi wasallam) ankati akakhudzidwa ndi mavuto azachuma, Mtumiki (Swallallah alayhi wasallam) ankawalimbikitsa kuthetsa mavuto awo kudzera mu swalah ndipo amawerengera vesi yomwe ili pamwambayi.
Chipilala chachikulu mu Diin
Munthu ankati akalowa chisilamu mwazinthu zoyambilira zimene Mtumiki Swallallah alayhi wasallam ankamuphunzitsa ndi Swalaah.
Mtumiki swallallahu alaihi wasallam moyo wake onse adadzipereka polimbikitsa swalah pakati pa ummah wake. Pamene adafika ku Quba ndi Madinah Munawwarah, chinthu chake choyamba chapamwamba kuposa zonse kunali kumanga mzikiti komanso kwalimbikisa anthu zaswalah.
Kupatula zimenezi, Mtumiki Swallallah alayhi wasallam adalamula kuti mzikiti umangidwe mdera lililonse pofuna kuwalumikizitsa anthu kudzera mu swalah
Mtumiki Swallallah alayhi wasallam adati, “Swalaah ndichipilala chapakati pa deen.” Mkunena kwina tinganene kuti, kudzera mukuteteza chipilala chimenechi, ndiye kuti munthu dini yake yonse idzakhala yotetezedwa, ndipo kudzera mukuononga chipilala chapakatichi ndiye kuti dini yonse yamunthu idzaphwasuka.
Olemekezeka Aaishah Radhwiyallahu anha akufotokoza chikhalidwe cha Mtumiki Swallallah alayhi wasallam ndi ubwino umene adawonetsa opemphelera swalah kumzikiti. Aishah Rdhwiyallahu anha akufotokoza kuti, “Mnyumba Mtumiki Swallallah alayhi wasallam nthawi zonse amathandizira kugwira ntchito zapakhomo. Komano amati akangomva adhaana pompopompo amanyamuka m’nyumbamo kumapita kumzikiti.
Nthawi ina yake, Gulu lapaulendo lochokera fuko la Thaqiif lidabwera kwa Mtumiki Swallallah alayihi wasallam ndicholinga chodzalowa chisilamu. Koma anamupempha Mtumiki kuti asamapite kujihadi, asamapereke chakhumi cha zakati kwa anthu otolera zakati komanso kuti asamaswali.
Mtumiki Swallallah alayhi wasallam adavomereza mapempho awiri oyambawo komano adakana kuwapatsa chilorezo chosiya kupemphera swalah. Mtumiki Swallallah alayhi wasallam adati “Palibe ubwino pachipembedzo pamene swalah ikusiyidwa.”
Kufunikira kwa Swalaah pa Moyo Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anhu)
Kufunika ndi kufunikira kwa Swalah kudakhanzikika kwambiri m’mitima ya ma Swahaabah (Radhwiyallahu anhum) kotero kuti ngakhale pa nthawi imene adali atatsala pang’ono, ankaonetsetsa kuti achirimika pa nsanamira ya Swalaah.
M’mawa omwe Umar (Radhwiyallahu anhu) adabayidwa, Miswar bin Makhramah (Radhwiyallahu anhu) atafika pamaso pake, Atalowa adampeza Umar (Radhwiyallahu anhu) ali chikomokere.
Miswar (Radhwiyallahu anhu) adawafunsa omwe adalipo pamalopo ngati Umar (Radhwiyallahu anhu) anaswali. Adayankha kuti sadatsitsimuke, zachidziwikire kuti sanaswali.
Miswar (Radhwiyallahu anhu) ankadziwa kufunikira kwa swalah kwa Umar (Radhwiyallahu anhu) moyo wake onse. Choncho Miswar adawalangiza kuti amudzutse pomudziwitsa kuti ndi nthawi ya Swalah. Choncho adaitana kunena kuti: “E Amiirul Mu’mineen, Swalah!”
Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anhu) atangomva mawu oti swalah adadzuka nati: “Inde! Ndikulumbira mwa Allah! Palibe gawo mu chisilamu kwa iwo amene amanyalanyaza Swalah yawo!” Umar pambuyo pake adaswali Swalah yake.
Umar (Radhwiyallahu anhu) adafunsanso: “Kodi anthu aswali Swalah yawo ya Fajr?” Adauzidwa kuti aswali Swalah yawo. Apa ndi pamene Umar adakhutitsidwa.”
Tipemphe Allah kuti atikhazikitse pa Swalaah ndi kutipatsa mphamvu zotsatira Sunnah iliyonse ya Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) m’mnyengo zonse za moyo.