Kulandira dzina loti ‘Mthandizi Wapadera’ wa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Pankhondo ya Ahzaab, yomwe imadziwikanso kuti Nkhondo ya Khandaq (Nkhondo ya Ngalande), Asilamu adalandira uthenga kuti Banu Quraizah adaswa lonjezo lawo loti adzakhulupirika kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo adajoina adani. Kuti atsimikize zomwe zamvekazi, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawafunsa ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) kuti: “Ndani andibweretsere nkhani za anthu awa (Banu Quraizah)?” Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adayankha nthawi yomweyo ndikudzipereka kuti apita ngati kazitape ndikubweretsa uthenga wa Banu Quraizah kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam).

Patapita nthawi, Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adafunsanso kuti: “Ndani andidziwitse za anthu awa (Bani Quraizah)?” Apanso, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adadzipereka kupita. Pomaliza, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adafunsanso kachitatu kuti: “Ndani andibweretsere uthenga wa anthu awa (Banu Quraizal?) Pamenepa Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adadzipereka kuti apita. Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adasangalala kwambiri ndi kusangalatsidwa ndi Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo ananena kuti, “Ndithu Nabi aliyense adali ndi mthandizi wapadera, ndipo mthandizi wanga wapadera ndi Zubair bin ‘Awwaam (Radhwiyallahu “anhu” (Siyar A’ laam min Nubalaa 3/30, Saheeh Bukhaari #1719, Sahihul Muslim #2415, Sunan Tirmizi #1745, Fat-hul Baari 6/63, 7/100)

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …