Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga 3

6. werengani Surah Sajdah musanagone.

Olemekezeka Jaabir (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) sankagona mpaka atawerenga Surah Sajdah ndi Surah Mulk.[1]

Khaalid bin Ma’daan rahimahullah, Taabi’ee, adatchula izi: “Ndithu Surah Sajdah idzakangana m’manda poteteza amene ankaiwerenga. Idzati, ‘O, Allah! Ngati ndili ochokera ku chitaab Chanu, muvomereni chiwombolo changa kwa iye, ndipo ngati sindiri wa mchitaab Chanu, ndifufuteni mmenemo!’ Surayi idzatenga mawonekedwe a mbalame ndipo idzatambasura mapiko ake pamwamba pake (kuti imuteteze). Idzampempherera ndi kumteteza ku chilango cha kumanda, ndipo Surah Mulk nayonso ili ndi ma ubwino abwino omwewo.” Zanenedwa kuti chifukwa cha ubwino wamtengo wapatali umenewu, Khaalid bin Ma’daan rahimahullah ankaonetsetsa kuti asakagone mpaka atawerenga Sura Sajdah ndi Surah Mulk. [2]

7. Werengani Surah Dukhaan usiku wa Lachinayi (usiku wa Jumaa).

Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alihai wasallam) adati: “Amene adzawerenge Surah Haa miim Ad-Dukhaan usiku wa Jumu’ah (lomwe ndi: Lachinayi usiku), machimo ake onse adzakhululukidwa.”[3]

Abu Umaamah (Radhwiyalahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene wawerenga Sura ya Dukhaan usiku otsatizana ndi lachisanu (lachinayi madzulo) kapena Lachisanu, Allah adzam’mangira nyumba yachifumu ku Jannah.[4]

8. Werengani Surah Kahf tsiku la Jumu’ah.

Ibnu Umar (Radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene amawerenga Surah Kahf tsiku la Jumu’ah, kuwala kumachokera pansi pa mapazi ake ndi kupita kumwamba. Nuur iyi idzamuunikira pa tsiku la Qiyaamah, ndipo adzakhululukidwa machimo ake onse (ang’ono) amene adachita pakati pa Jumu’ah ziwiri.”[5]

Ali (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene angawerenge Surah Kahf tsiku la Jumu’ah (ndi kukwaniritsa malamulo a Jumu’ah), Allah adzamuteteza kwa masiku asanu ndi atatu ku fitnah iliyonse. Ngati zingachitike kuti Dajjaal ndikutulukira (m’masiku asanu ndi atatu a chitetezo cha Allah wa), munthu ameneyo adzatetezedwa kwa iye (Dajjaal).”[6]

Abu Sa’iid Khudri (Radhwiyallahu anhu) akunena kuti: “Munthu amene amawerenga Surah Kahf tsiku la Jumu’ah, ngati atakumana ndi Dajjaal, ndiye kuti Dajjaal sadzatha kumugonjetsa kapena kumuvulaza.[7]


[1] سنن الترمذي، الرقم: 2892، وقال الحاكم في المستدرك 2/446: هذا حديث صحيح على شرط مسلم ولم يخرجه لأن مداره على حديث ليث بن أبي سليم عن أبي الزبير وأقره الذهبي

[2] سنن الدارمي، الرقم: 3453، وإسناده ضعيف

[3] سنن الترمذي، الرقم: 2889، وقال: هذا حديث غريب لا نعرفه إلا من هذا الوجه وعمر بن أبي خثعم يضعف قال محمد وهو منكر الحديث

[4] المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 8026، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله في مجمع الزوائد، الرقم: 3017: رواه الطبراني في الكبير وفيه فضال بن جبير وهو ضعيف جدا

[5] رواه أبو بكر بن مردويه في تفسيره بإسناد لا بأس به كذا في الترغيب والترهيب، الرقم: 1098

[6]  المختارة للضياء المقدسي، الرقم: 429

[7] شعب الإيمان، الرقم : 2776، وقال الحاكم في المستدرك، الرقم: 8562 هذا حديث صحيح الإسناد ولم يخرجاه وقال الذهبي: صحيح

Check Also

Nthawi Zomwe Ma Dua Amayankhidwa

Nthawi ya Azaan ndi Pamene Magulu Awiri Akumana Pankhondo Olemekezeka Sahl bin Sa’d (Radhwiyallahu anhu) …