Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga 2

4. Werengani Surah Yaasiin m’mawa ndi madzulo aliwonse.

Ibnu Abbaas (Radhwiyallahu anhu) adati: “Amene angawerenge Surah Yaasiin m’bandakucha, ntchito yake ya tsiku lonse idzafewetsedwa, ndipo amene angaiwerenge madzulo, ntchito yake mpaka m’mawa idzafewetsedwa.”[1]

Olemekezeka Jundub (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anati: “Amene angawerenge Surah Yaasiin usiku ndi cholinga chofuna kusangalatsa Allah, machimo ake (ang’onoang’ono) adzakhululukidwa.” [2](Mu hadith ya Shu’abul Imaan kwatchulidwa kuti amene angawerenge Surah Yaasiin, adzakhululukidwa machimo ake ang’onoang’ono, Hadith iyi siikufotokoza nthawi yeniyeni yowerenga, utha kuwerenga masana kapena usiku.[3]

5. Werengani Surah Mulk musanagone.

Kwanenedwa kuti Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu anhu) adati: “Amene amawerenga Surah Mulk usiku uliwonse, ndiye kudzera mukuwerenga surayi, Allah adzamuteteza ku chilango cha m’manda. M’nthawi ya Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) tinkaitcha surayi ndi dzina lakuti ‘Al Maani’ah (yomwe imateteza munthu ku chilango cha m’manda)’. Ndithu, iyi ndi surah yoti, Amene akuiwerenga usiku uliwonse, amapindula kwambiri, ndipo amakhala kuti wachita zabwino. “[4]

Mtumiki (Swallallahu Alaihi Wasallam) adanena za Surah Mulk kuti: “Ndikukhumba (Surah Mulk) kuti ikhale pamtima pa munthu aliyense mu Ummah wanga.[5]

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu Alaihi Wasallam) adati: “Ndithu, pali surah yaikulu ya Qur’an Majiid yomwe ili ndi ma aya makumi atatu. Idzampembedzera munthu (yemwe akuiwerenga mosunga nthawi) mpaka atakhululukidwa. Sura iyi ndi Surah Tabaarak.”[6]


[1] سنن الدارمي، الرقم: 3462، وفي سنده ضعف

[2] صحيح ابن حبان، الرقم: 2574

[3] شعب الإيمان، الرقم:2235، وقال الصنعاني في التنوير 10/353: رمز المصنف لضعفه

[4] عمل اليوم والليلة للنسائي، الرقم: 711، وقال العلامة المنذري رحمه الله في الترغيب والترهيب، الرقم: 2453: رواه النسائي واللفظ له والحاكم وقال: صحيح الإسناد

[5] المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 11616، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله في مجمع الزوائد، الرقم: 11429: رواه الطبراني وفيه إبراهيم بن الحكم بن أبان وهو ضعيف

[6] سنن الترمذي، الرقم: 2891، وقال: هذا حديث حسن

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …