Kusamalitsa pofotokoza Hadith yochokera kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam)

Abdullah bin Zubair (Radhwiya Allaahu ‘anhu) akuti nthawi ina adafunsa bambo ake (omwe ndi) Zubair radhwiyallahu ‘anhu kuti, “Bwanji simumafotokoza ma haadiith a Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), monga momwe amachitira ma Swahaabah ena (Radhwiyallahu anhum)?”

Olemekezeka Zubair (Radhwiya Allahu ‘anhu) anayankha kuti, “Sindinachokepo kumbali ya Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) kuyambira pomwe ndidalowa Chisilamu (le. Ine nditha kukwanitsa kufotokoza mahaadiith ambiri kuchokera kwa iye). Koma kuti, nthawi ina, ndinamumva Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). akutchulapo kanthu (chifukwa chomwe amachitira mantha kufalitsa ma haadiith, ndinamva Mtumiki (Swallallaahu ‘alaih wasallam) akunena kuti: “Amene wandinamizira mwadala (kupeka ma haadiith ndi kumanena kuti ndi mawu anga) akonzekere kuti nyumba yake ndi kugahena.”

Check Also

Kuwolowa manja ndi Zuhd (Kudzipatula padziko lapansi) kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu)

Nthawi ina, Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adatenga ndalama za golide mazana anayi, naziika m’thumba napereka …