binary comment

Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga 4

9. Werenganinso ayah zitatu zomaliza za Surah Baqarah musanagone.

Kwanenedwa kuti Ali (Radhwiyallahu anhu) adati: “Sindikuganiza kuti aliyense wanzeru angagone popanda kuwerenga ma aya (atatu) omaliza a Surah Baqarah, chifukwa ndithu iwowo ndi chuma chochokera pansi pa Arsh.

10. Werengani Surah Faatihah ndi Surah Ikhlaas musanagone.

Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaih wasallam) adati: “(Pa nthawi yogona) ukaika nthiti zako pabedi, ndipo wawerenga Surah Faatihah ndi Surah Ikhlaas, udzakhala otetezeka ku chilichonse kupatula imfa.

11. Werenganinso Surah Zumar ndi Surah Bani Israaeel musanagone.

Abu Lubaabah (Rdhwiyallahu anhu) adasimba kuti Bibi Aaishah (Radhwiyallahu anha) adati: “Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) sankagona mpaka atawerenga Surah Zumar ndi Surah Bani Isra’eel.

12. Werenganinso mawu a musabbihaat (i.e. surah zomwe zimayamba ndi mawu a Tasbeeh) musanagone.

Sura zimenezi ndi Surah Bani Israaeel, Surah Hadeed, Surah Hashr, Surah Saff, Surah Jumu’ah, Surah Taghaabun ndi Surah A’ala. Irbaadh bun Saariyah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) sankagona mpaka atawerenga ma Musabbihaat, ndipo amati: “M’surayi muli ayah yabwino kwambiri kuposa aya chikwi chimodzi.


[1] سنن الدارمي، الرقم: 3427، وأخرج الإمام ابن أبي داود بإسناد صحيح على شرط البخاري ومسلم عن علي – كرم الله وجهه – موقوفا: ما كنت أرى أحدا يعقل ينام قبل أن يقرأ الآيات الثلاث الأواخر من البقرة كذا في مرقاة المفاتيح 4/1668

[2] مسند البزار، الرقم: 7393، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله في مجمع الزوائد، الرقم: 17030: رواه البزار وفيه غسان بن عبيد وهو ضعيف ووثقه ابن حبان وبقية رجاله رجال الصحيح

[3] سنن الترمذي، الرقم: 3405، 2920، وقال: هذا حديث حسن غريب

[4] سنن الترمذي، الرقم: 3406، وقال: هذا حديث حسن غريب

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 1

1. Yambani dua pomulemekeza Allah kenako mudzamuwerengera duruud Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Pambuyo pake, modzichepetsa …