Kukhazikika pa Chisilamu

Abul Aswad akusimba motere. Olemekezeka Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adamulandira Chisilamu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu, ndipo adapanga Hijrah ali ndi zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu. Amalume ake ankamukulunga munkeka ndikumampepelera utsi kuti abanike. Kenako ankamulamula kuti asiye Chisilamu ndipo iye ankayankha kuti: “Sindidzakhala Kaafir!

Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) anali m’gulu la ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) amene adapanga Hijrah kupita ku Abyssinia kuthawa mazunzo a ma Quraish. Komabe, sadakhale nthawi yayitali ku Abyssinia, mpaka adabwerera ku Makkah Mukarramah ndipo kenako adapita ku Madinah Munawwarsh. Choncho adadalitsidwa ndi mwayi ochita nawo ma hijrah onse awiri chifukwa cha Chisilamu. (Tahzeeb ul-Kamaal 9/321, Siyar Alsam man Nubeloa 3/30)

AUD-20240718-WA0002

Check Also

Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu) Apereka Uphungu kwa Mtsogoleri wa Asilikali Kuti Atsatire Chilungamo

Imaam Bayhaqi (rahimahullah) akunena kuti: Yazid bin Abi Sufyaan (radhiyallahu ‘anhu) pamene adali bwanamkubwa wa …