Hishaam bun Urwah akufotokoza kuti ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) okwana asanu ndi awiri adamusankha Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti adzatenge udindo ogawa chuma chawo akadzamwalira. Ena mwa ma Swahaabawa anali Olemekezeka Abdur Rahmaan bin ‘Auf (Radhwiyallahu ‘anhu), Olemekezeka Miqdaad (Radhwiyallahu anhu) ndi Olemekezeka Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu ‘anhu) atamwalira, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adatenga udindo ogawa chuma chotsala komanso adasamalira chuma cha ana awo ndiponso ankathandiza anawo pogwiritsa ntchito chuma chake. (Usul Ghasbah 2/211).
Check Also
Mantha a Abdur Rahman bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) kuyankha mlandu ngakhale adawonongera chuma pa ntchito ya Dini.
Shu’bah (Rahimahullah) akuti: Nthawi ina Abdur Rahman bun Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) ankasala kudya ndipo nthawi …