Kufunika Kwa Dua 3

Njira Yopezera madalitso Ndi kudzitetezera Kwa Adani

Olemekezeka Jaabir bin Abdillah akusimba kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adauza maSwahaabah kuti: “Kodi sindingakusonyezeni njira yoti mupulumutsidwe kwa adani anu ndi kulandira zochuluka m’zimene muli nazo? Tembenukirani kwa Allah usiku ndi usana chifukwa dua ndi chida cha okhulupirira.”[1]

Mngelo Apangira Dua Munthu Yemwe Amapangira Dua M’bale wake

Olemekezeka Abud Dardaa adanena kuti Rasulullah ankanena kuti: “Dua yomwe Msilamu amachitira m’bale wake iye kulibe, ndiyovomerezeka. Nthawi zonse akamuchitira m’bale wake zdua yabwino, pamakhala mngelo oikidwa kuti amuyime pamutu pake. Mngelo oikidwayu amanena Aameen ku dua yake ndipo mngelo amamupemphera kwa Allah kuti: ‘Allah akupatse zofanana ndi zomwe wampemphera m’bale wako.[2]

Ubwino Owapangira Dua Anthu Okhulupirira (Asilamu)

Abud Dardaa (Radhwiyallahu anhu) adanena kuti adamumva Mtumiki (Swallallahu alaiji wasallam) akunena kuti: “Amene wawapemphera chikhululuko kwa Allah amuna ndi akazi kokwana makumi awiri ndi zisanu (25) kapena makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri (27) tsiku lililonse, adzakhala mgulu la anthu amene ma duwa awo ayankhidwa (ndi Mulungu) ndipo adzakhala m’gulu la akapolo oopa Mulungu chifukwa cha ntchito zawo zabwino zomwe Mulungu watsitsira riziki pa dziko lapansi.[3]

AUD-20240723-WA0014


[1] مسند أبي يعلى الموصلي، الرقم: 1812، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله في مجمع الزوائد، الرقم: 17199: رواه أبو يعلى وفيه محمد بن أبي حميد وهو ضعيف

[2] صحيح مسلم، الرقم: 2733

[3] رواه الطبراني وفيه عثمان بن أبي العاتكة وقال فيه: حدثت عن أم الدرداء وعثمان هذا وثقه غير واحد وضعفه الجمهور وبقية رجاله المسمين ثقات كذا في مجمع الزوائد، الرقم: 17600

Check Also

Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 2

Munthu Yemwe Akudwala Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anahu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mukakumana …