Kulimba Mtima kwa Zubair (Radhiyallahu ‘anhu)

Patsiku la (nkhondo) ya Yarmuuk, ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) adati kwa Zubair (Radhiyallahu ‘anhu): “Bwanji siukupita ndi kukamenyana ndi adani, ndipo ife tidzakutsatira pokalimbana ndi adani.?”

Zubair (Radhwiya Allahu ‘anhu) adayankha: “Ndikudziwa kuti ngati ndingapite anthu inu simungagwirizane nane.”

Ma Swahaabah (Radhiyallahu ‘anhum) adati: “Ayi, ife tikugwirizana nawe ndipo tikutsatira.”

Choncho Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adalowelera m’ mizere ya adani omwe adawaukira. Adapitirizabe kumenyana nawo adaniwo mpaka adafika kumapeto kwa mbali ya adaniwo ndipo palibe m’modzi mwa an zake omwe adamuphatira kufikira pamenepa.

Ndipo atabwerera (kumbali ya Msilamu), adani adagwira Chingwecha kavalo wake, ndipo adamumenya kawiri (Ndi malupanga awo) paphewa pake. Kupatula mabala awiriwa (amene adavulala pankhondo ya Yarmuuk), padalinso bala lina pakati pa mabala awiriwa omwe adalipo chifukwa cha kumenyedwa ndi lupanga pa nkhondo ya Badri.

Urwah (rahimahullah) pofotokoza zomwe zili pamwambazi adati: “Ine ndiri mwana, ndikusewera, ndinkalowetsa zala zanga m’mabowo (a khungu la phewa lake).

Tsiku limenelo (la Yarmuuk, mchimwene wanga) Abdullah bin Zubair nayenso adali nawo (bambo athu, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu)) ndipo adali ndi zaka khumi panthawiyo. Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adamukweza pahatchi ndikusankha munthu oti amuyang’anire (panthawi ya nkhondo). (Saheeh Bukaari #3975)

AUD-20240730-WA0000

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …