Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 1

Makolo, Wapaulendo ndi Oponderezedwa

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ma dua atatu ndi otero kuti pangavute bwanji adzalandiridwa; dua ya bambo (kapena mayi, pa mwana wawo), dua ya musaafir (munthu wapaulendo) komanso dua ya oponderezedwa.”[1]

Munthu Osala kudya komanso Mtsogoleri Wachilungamo

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Anthu atatu maduwa awo sangakanidwe; osala kudya kufikira atamasura swaum yake, mtsogoleri wachilungamo, ndi dua ya munthu oponderezedwa imene Allah amaikweza m’mwamba kumitambo, ndi imene makomo akumwamba amatsegulidwa, ndipo Allah amanena kuti: ‘Ndikulumbilira ulemerero wanga! Ndithu ndikuthandiza ngakhale patapita nthawi!’[2]

Mujaahid (Nsilikali) komanso Yemwe akuchita Haji kapena Umrah

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) adasimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mujaahid komanso amene akuchita Haji ndi umrah ndi nthumwi za Allah. Ngati amupempha Allah Iye amayankha mapemphero awo ndipo ngati apempha kanthu kwa lye, amawapatsa.”[3]

AUD-20240731-WA0013


[1] سنن الترمذي، الرقم: 3448، وقال: هذا حديث حسن

ولم يذكر الوالدة لأن حقها أكثر فدعاؤها أولى بالإجابة (مرقاة المفاتيح 4/1535)

[2] سنن الترمذي، الرقم: 3598، وقال: هذا حديث حسن

[3] سنن أبي داود، الرقم: 1535، سنن الترمذي، الرقم: 1980، وقال: هذا حديث غريب لا نعرفه إلا من هذا الوجه والأفريقي يضعف في الحديث

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …