Olemekezeka Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adanenapo kuti:
“Ndithu, Talhah bin ‘Ubaidillah (Radhwiyallahu ‘anhu) amasunga mayina a Ambiyaa (‘alaihimus salaam) kwa ana ake, pomwe akudziwa kuti sipadzakhala Nabiy odzabwera pambuyo pa Mtumiki Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam).
Zubair (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adati: “Ndimasungira ana anga maina a mashahidi (achi Swahaabah) kuti mwinanso ana anga adzadalitsidwe nawo
kuphedwa munjira ya Allah.”
Choncho Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) anamutcha mwana wake Abdullah dzina la Abdullah bin Jahsh (Radhwiyallahu ‘anhu) (yemwe adaphedwa pankhondo ya Uhud).
Anamutcha mwana wake Munzir kuchokera kwa Munzir bun Amr (Radhwiyallahu ‘anhu) (yemwe adaphedwa ku ya Biru Mauunah).
Anamutcha mwana wake Urwah dzina la ‘Urwah bin Mas’uud (Radhwiyallahu ‘anhu) (yemwe adaphedwa ndi anthu ake atawaitanira ku Chisilamu).
Anamutcha mwana wake Hamzah kuchokera kwa Hamzah bin Abdil Muttalib (Radhwiyallahu ‘anhu) (yemwe adaphedwa pankhondo ya Uhud).
Adamutcha mwana wake Ja’far kuchokera kwa Ja’far bun Abi Taalib (Radhwiyallahu ‘anhu) (yemwe adaphedwa pankhondo ya Mu’tah).
Anamutcha mwana wake Mus’ab dzina la Mus’ab bun “Umair (Radhwiyallahu ‘anhu) (yemwe adaphedwa pankhondo ya Uhud).
Adamutcha mwana wake Ubaidah dzina la “Ubaidah bin Haarith (Radhwiyallahu ‘anhu) (yemwe adaphedwa pankhondo ya Badri).
Adamutcha mwana wake Khaalid dzina la Khaalid bun Said (Radhwiyallahu ‘anhu) (yemwe adaphedwa pankhondo ya Marjus Safar kapena Ajnadiin).
Adamutcha mwana wake ‘Amr kuchokera kwa ‘Amr bun Said bin ‘Aas (Radhwiyallahu ‘anhuma) yemwe anaphedwa pa nkhondo ya Yarmuk. (Tabaqaat ibn Sa’d 3/74)