Munthu Yemwe Akudwala
Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anahu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mukakumana ndi odwala, mupempheni kuti akupangireni duwa chifukwa dua yake ili ngati dua ya angero (chifukwa cha kudwalako, machimo ake amakhululukidwa), choncho akufanana ndi angelo pokhala opanda machimo, ndipo potero pempho lake lidzalandiridwa mwachangu).
Yemwe Amapanga Dua Pamavuto
Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahuanhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene akufuna kuti Allah ayankhe duwa yake panthawi imene iye ali pamavuto, achulukitse maduwa nthawi imene ali ntendere ochuluka.
Yemwe Amathandiza Mzake pa Zachuma
Olemekezeka Ibnu Umar (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene akufuna kuti duwa yake iyankhidwe ndi kuchepetsa vuto lake, ayenera kumuthandiza nzake yemwe ali m’mavuto azachuma.”
[1] سنن ابن ماجه، الرقم: 1441، وقال العلامة البوصيري رحمه الله في مصباح الزجاجة (2/21): هذا إسناد رجاله ثقات إلا أنه منقطع قال العلائي في المراسيل والمزي في التهذيب أن رواية ميمون بن مهران عن عمر مرسلة
[2] سنن الترمذي، الرقم: 3382، وقال: هذا حديث غريب
[3] مسند أحمد، الرقم: 4749، ورجال أحمد ثقات كما في مجمع الزوائد 4/133