Kudalirika Kwenikweni Kwa Olemekezeka Abu Ubaidah bin Jarrah (Radhwiyallahu ‘anhu)

Anthu a ku Najraan atalowa Chisilamu, adadza kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) namupempha kuti awatumizire munthu odalirika (yemwe angakawaphunzitse Swalah). Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa iwo:

لأبعثن إليكم رجلا أمينا حق أمين

Ndidzatumizirani munthu okhulupirira ndi odalirika kwambiri.

Pa nthawiyo, ma Swabsaabah (Radhwiyallahu anhum) omwe adalipo onse ankalakalaka kuti akalandire nkhani yabwinoyi kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). Kenako Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamusankha Abu Ubaidah (Radhwiya Allahu ‘anhu) kuti apite kwa anthu a ku Najraan kukawaphunzitsa Dini.

Abu Ubaidah (Radhwiya Allaahu ‘anhu) atayimilira kuti adzichoka, Mtumiki Swallallahu ‘alaihi wasallam) adanena mawu okamba za iye kuti, “Munthu uyu ndi odalirika (wapaderadera) mu Ummah uno” (Swahiyh Bukhaariy #3480-3481).

Chidziwitso: Khalidwe losonyeza kudalirika linali chizindikiro cha ma Swahaabah onse. Komabe, chifukwa chakuti khalidweli linali lapamwamba kwambiri pa moyo wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu), Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adampatsa udindo wapadera umenewu.

AUD-20240812-WA0007

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …