Khumbo la Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kudalitsidwa ndi Chipinda Chodzaza ndi Anthu monga Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) nthawi ina anakhala pansi ndi gulu la maswahabah pamene iye analankhula nawo ndipo kenako anafunsa funso lonena kuti, “Tandiuzani chimene anthu inu mukulakalaka”

Munthu wina adati: “Chokhumba chomwe ndili nacho ndikuti chipinda chonsechi chitadzadza ndi ma dirham (ndalama zasiliva) ndikuti ndiwononge zonsezo panjira ya Allah Ta’ala.”

Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adayankhulanso ndikuwafunsanso kachiwiri: “Ndiuzeni chomwe mukulakalaka anthu inu!”

Munthu wina adati: “Khumbo lomwe ndiri nalo ndikuti chipinda chonsechi chitadzadza ndi ndalama za golide, ndipo zonsezo ndikuzipereka panjira ya Allah Ta’ala.

Apanso Umar (Radhwiyallahu ‘ adawafunsanso funso lomwelo, “Ndiuzeni chomwe mukkhumba anthu inu!”

Munthu wachitatu adati: “Chokhumba chimene ndili nacho ndi chakuti chipinda chonsechi chidzazidze ndi miyala yamtengo wapatali ndipo ndiigwiritse ntchito yonse panjira ya Allah Taala.

Umar (Radhwiyallahu ‘anhul adafunsanso funso lomweli kachinayi ndikufunsa ngati pali wina ali ndi chikhumbo lilichonse, koma adayankha kuti sadafune china chilichonse.

Kenako, olemekezeka Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adafotokoza khumbo lake nati: “Khunbo lomwe ndiri nalo ndikuti chipindachi chidzadze ndi amuna otere, omwe ali ngati Abu Ubaidah, Mu’aaz bin Jabal ndi Huzaifah bin Yamaan (Radhwiyallahu ‘anhum) kotero kuti nditha kugwiritsa ntchito aliyense wa iwo mu kumvera kwa Allah Ta’ala. Nditha kuzigwiritsa ntchito potumikira Dini ndikufalitsa Dini padziko lapansi.

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …