Nthawi Zomwe Ma Dua Amayankhidwa

Nthawi ya Azaan ndi Pamene Magulu Awiri Akumana Pankhondo

Olemekezeka Sahl bin Sa’d (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adati: “Pali nthawi ziwiri zomwe madua sangakanidwe kapena nthawi zambiri sangapande osayankhidwa; pa nthawi ya Azaan ndi pamene magulu awiri ankhondo akumana pankhondo.”[1]

Pakati pa Azaan ndi Iqaamah

Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Dua yomwe imapangidwa pakati pa Azaan ndi Iqaamah siimakanidwa.”[2]

Pakati pa Usiku

Olemekezeka Uthmaan bun Abil Aas Thaqafi (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Zitseko zakumwamba zimatseguridwa likadutsa theka la usiku. Kenako mngelo amafunsa kuti: ‘Kodi alipo amene akupempha kuti dua yake iyankhidwe? Kodi pali wina aliyense opempha kuti amupatse chomwe wapempha? Kodi alipo amene ali m’mabvuto kuti achepetsedwe mavuto ake?’ Pambuyo pake, palibe Msilamu amene amapempha kwa Allah kupatula kuti Allah amayankha mapemphero ake, kupatula wachigololo kapena munthu olanda chuma cha anthu mokakamiza.”[3]

AUD-20240820-WA0014

Dua pambuyo pa Swalah ya Fardh ndi nthawi ya Tahajjud

Olemekezeka Abu Umaamah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti nthawi ina, Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adafunsidwa kuti: “Ndi dua iti yomwe imalandiridwa (ndi kuvomerezedwa)?” Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adayankha: “Dua yochitidwa kumapeto kwa usiku ndi pambuyo pa swalah ya fardh.”[4]


[1] سنن أبي داود، الرقم: 2540، وسكت عنه هو والمنذري في مختصره

[2] سنن أبي داود، الرقم: 521، سنن الترمذي، الرقم: 212، وقال: حديث أنس حديث حسن

[3] المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 8391، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله في مجمع الزوائد، الرقم: 17245: رواه الطبراني ورجاله رجال الصحيح

[4] سنن الترمذي، الرقم: 3499، وقال هذا حديث حسن

Check Also

Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 2

Munthu Yemwe Akudwala Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anahu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mukakumana …