Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri a chisoti chake chachitsulo chovala pankhondo adalowa mmatsaya ake odalitsika.

Abu Bakr Siddiiq (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) nthawi yomweyo anathamanga kukamuthandiza Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) anayamba kuzula manowo ndi mano ake. Pamene limodzi mwa mano ake linachotsedwa, anali atagwerukanso dzino. Mosanong’oneza bondo kuti dzino lake lagweruka , anagwiritsanso ntchito mano ake kuzulanso dzino lina lachisoti. Anakwanitsa kuchotsa dzino lina, komabe m’menemo, anahwerukanso dzino lina.

Pamene mano achisotiwo adachotsedwa, magazi adayamba kutuluka m’thupi la Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alaihi wasallam). Malik bun Sinaan (Radhwiyallahu ‘anhu), bambo ake a Abu Sa’iid Khudri (Radhwiyallahu ‘anhu), adatsatira magaziwo ndi mfundo yake. Pazimenezi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Moto wa Jahannama siudzatha kukhudza munthu amene asakanikirana magazi anga ndi ake.” (Musnad Abi Dawood Tayaalisi #6 & Fathul Baari 7/366)

Check Also

Khumbo la Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kudalitsidwa ndi Chipinda Chodzaza ndi Anthu monga Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) nthawi ina anakhala pansi ndi gulu la maswahabah pamene iye analankhula nawo …