Zichitochito za Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Zigwirizana ndi Quraan Majiid

Pankhondo ya Badr, bambo a Abu Ubaidah Radhwiyallahu anhu adapitiriza kumulondora kufuna kuti amuphe. Komabe, iye anapitirizabe kuwapewa bambo akewo kuti asakumane nawo n’kuwapha.

Komabe, iwowa atayesetsa ndikukumanizana naye maso ndi maso ndipo panalibe njira ina yopulumutsira moyo wake koma kuwapha, iye anapita patsogolo ndi kuwapha.

Apa ndipamene Allah Taala adavumbulutsa ndime iyi:

لَّا تَجِدُ قَوْمًا يُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ يُوَادُّونَ مَنْ حَادَّ اللَّهَ وَرَسُولَهُ وَلَوْ كَانُوا آبَاءَهُمْ أَوْ أَبْنَاءَهُمْ أَوْ إِخْوَانَهُمْ أَوْ عَشِيرَتَهُمْ ۚ

“Simudzapeza anthu amene akhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro ali ndi chikondi pa anthu amene akutsutsana ndi Allah ndi Mtumiki Wake (Swallallaahu ‘alayhi wasallam), ngakhale anthuwo atakhala abambo awo, ana awo, achibale awo kapena anthu akumtundu kwawo.” (Surah Mujaadalah v22) (Majma’uz Zawaaid #14906)

Check Also

Khumbo la Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kudalitsidwa ndi Chipinda Chodzaza ndi Anthu monga Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) nthawi ina anakhala pansi ndi gulu la maswahabah pamene iye analankhula nawo …