binary comment

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 1

1. Yambani dua pomulemekeza Allah kenako mudzamuwerengera duruud Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Pambuyo pake, modzichepetsa ndi ulemu onse, mudzapempha zosowa zanu pamaso pa Allah.

Olemekezeka Fadhaalah bin Ubaid (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti nthawi ina Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adakhala munzikiti pamene munthu wina adalowa ndikuyamba kuswali. Kenako adapempha nati: “Oh, Allah, ndikhululukireni ndipo ndichitireni chifundo.” Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adamuuza kuti: “E, iwe Musalli! Ukamaliza Swalah, ukakhala pansi (choyamba) mutamande Allah ndi matamando oyenelera ukulu Wake ndi ulemerero Wake. Pambuyo pake ndiwerengere duruud, ndipo pemphera kwa Allah ndipo mupemphe zofuna zanu.” Pambuyo pake, Mtumiki (Swallallahu alaih wasallam) adawona munthu wina akuswali. Atamaliza Swalah adachita dua. Poyamba adalemekeza Allah ndipo kenako adawerenga duruud pa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adamuuza kuti: “E, iwe Musalli, pemphera kwa Allah ndipo umpemphe zofuna zako, ndipo dua yako idzayankhidwa (popeza wakwaniritsa mfundo zoyenera kutsatira ukamafuna kupanga dua).”[1]

Olemekezeka Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu anhu) adati: “Aliyense wa inu akafuna kupemphera pamaso pa Allah mu dua, ayambe ndi kulemekeza Allah ndi kumtamanda ndi matamando oyenera ukulu Wake ndi ulemerero Wake. Pambuyo pake amuwerengere duruud Mtumiki (Swallallahu Alaihi Wasallam), kenako apemphere kwa Allah ndikupempha chimene wafuna. Ndithu (potsatira malamulo a dua) m’njira imeneyi, zikuyembekezeredwa kuti munthu adzapambana (kudzera mukuyankhidwa kwa dua yake).”[2]


[1] سنن الترمذي، الرقم: 3476، وقال: هذا حديث حسن وقد رواه حيوة بن شريح عن أبي هانئ الخولاني

[2]  المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 8780، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله في مجمع الزوائد 155/10: ورجاله رجال الصحيح إلا أن أبا عبيدة لم يسمع من أبيه

Check Also

Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 2

Munthu Yemwe Akudwala Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anahu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mukakumana …