Nthawi ina, Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adatenga ndalama za golide mazana anayi, naziika m’thumba napereka kwa wantchito wake: “Pita kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo ukampatse ndalamazi. Ukakafika kumeneko ukadikire kwa kanthawi kuti ukawone zomwe akachite ndi ndalamazo (ndipo ukabwerere ndikundidziwitsa).”
Kapoloyo anatenga thumba la ndalama za golide lija napita kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu). Adapereka mphatsoyo ponena kuti, “Ameerul Mu-miniin wanena kuti muyenera kugwiritsa ntchito izi pazosowa zanu.”
Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) adalandira mphatsoyo ndipo adamuoangira duwa Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti: “Allah Ta’ala amupatse kuyandikira Kwake kwapadera ndi kumuchitira chifundo”.
Atatero, anaitana kapolo wake natulutsamo timakobiri towerengeka ta golide m’thumbamo, nati, “Tenga makobidi asanu ndi awiri agolidi awa um’patse wina. Kenako anatulutsanso zina zowerengeka n’kunena kuti, “Pereka ndalama zagolide zisanuzi kwa munthu wakuti. Anapitiriza kutulutsa ndalama zagolide m’thumba n’kuzipereka kwa kapolo wake wamkazi, n’kumuuza kuti azipereka kwa anthu osiyanasiyana, + mpaka ndalama zonsezo zinatha.
Umar (radhiya Allahu ‘anhu) atamva za momwe Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) adagwiritsira ntchito ndalamazo kwa akapolo a Allah popereka sadaqa, adakondwera kwambiri.