Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu).

Olemekezeka Salmaan Faarsi (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: Ndithu Allah ndi olemekezeka, okoma mtima kwambiri komanso owolowa manja. Ulemu Wake ndiwakuti amaona kuti ndi zotsutsana ndi ukulu Wake ndi chifundo Chake kumusiya amene wakweza manja ake kwa Iye kuti apite chimanjamanja.”[1]

3. Pamene mukukweza manja anu kupanga dua, manja anu ayang’ane kumwamba.

Sayyiduna Maalik bun Yasaar (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Pomupempha Allah, mpempheni manja anu mutawayang’anitsa m’mwamba Musawayang’anitse pansi.

4. Siyani kampata pang’ono pakati pa zikhatho zanu (manja).

5. Pamene mukupanga dua, onetsani kulephera kwanu kotheratu, kusowa chochita ndi kufooka kwanu, ndipo mpempheni Allah ndi mawu ofewa ndi kudzichepetsa kotheratu.

وَاذْكُر رَّبَّكَ فِي نَفْسِكَ تَضَرُّعًا وَخِيفَةً وَدُونَ الْجَهْرِ مِنَ الْقَوْلِ بِالْغُدُوِّ وَالْآصَالِ وَلَا تَكُن مِّنَ الْغَافِلِينَ ‎﴿٢٠٥﴾‏

Ndipo mupemphe Mbuye wako modzichepetsa ndi mwa mantha ndi mopanda kukweza mawu m’bandakucha ndi madzulo. Ndipo usakhale mgulu la anthu osalabadira (malamulo a Allah).[2]


[1] سنن الترمذي، الرقم: 3556، وقال: هذا حديث حسن غريب

[2] سورة الأعراف: 205

Check Also

Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 3

Munthu Wachikulire Okhala ndi invi Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) …