Abdullah bin Marzuuq rahmatullah alaihi anali kapolo oopa Allah komanso anali m’nthawi ya ma Muhaddithiin akuluakulu monga Sufyaan bun Uyainah ndi Fudhail bun Iyaadh Rahimahumallah.
Poyamba, iye anali okonda moyo wa dziko lapansi ndipo sanali odzipereka ku Dini. Komabe, Allah adamudalitsa ndi tawfiiq (kuthekera) koti alape ndi kukonza moyo wake. Apa pakubwera nkhani ya kutembenuka kwake kwa mtima:
Tsiku lina Abdullah bin Marzuuq rahmatullah alaihi anali atatanganidwa ndi ntchito zoipa, kumwa mowa ndi kumvetsera nyimbo. Ali mkatikati mochita machimo amenewa, adaphonya Swalah yake ya Dhuhr, Asr ndi Maghrib.
Nthawi iliyonse ya Swalaah ikakwana, m’modzi mwa akapolo ake aakazi ankabwera kwa iye ndikumukumbutsa kuti aswali. Komabe, chifukwa cha kuledzera kwake ndi kutengeka kwake m’malcheza ndi zamsangulutso, iye sanalabadire uthenga wa mkaziyo.
Kenako, nthawi ya Esha Swalaah itatha ndipo usiku unatha, mdzakazi wakeyo anatenga nkhuni ya moto n’kuiika kuphazi kwake (kwa bwana wakeyo).
Mphamvu ya motoyo itamupeza, adakuwa chifukwa cha ululu ndikumufunsa mdzakaziyo kuti, “Ukutani!?” Kapoloyo anayankha kuti, “Pamene simungathe kupirira ku khala la moto pa dziko lino lapansi mudzaupilira bwanji moto waku Jahannam?
Atamva malangizo amenewa kuchokera kwa mdzakazi wake nthawi yomweyo anayamba kulira mofuula ichi chinali chiyambi cha kusintha kwa moyo wake.
Choncho adatembenukira kwa Allah ndi kuswali Swalah zomwe adaziphonya. Kenako anasintha moyo wake ndikusiya moyo wake wauchimo. Adapereka chuma chake m’njira ya Allah nayamba kukhala moyo ofewa, okwaniritsidwa ndi chuma chochepa chapadziko lapansi.
Pambuyo pokonzanso moyo wake, nthawi ina Sufyaan bun Uyainah rahmatullah alaih ndi Fudhail bun Iyaadh rahmatullah alaihi adamuyendera. Iwo adamupeza akukhala moyo osavuta omwe umagwirizana ndi Sunnah.
Sufyaan rahmatullah alaih adamufunsa kuti: “Mu Hadith zatchuridwa kuti munthu akapereka nsembe chifukwa cha Allah ndiye kuti Allah amam’bwezera zabwino koposa. Ndi chani chimene Allah wakupatsa pa nsembe yomwe mwapereka?”
Abdullah bin Marzuuq rahimahullah anayankha kuti: “Allah wandipatsa chisangalalo chenicheni ndi kukhutira kwa mtima.”
Kukumbukira Allah ndicho Chakudya cha Uzimu
Munthu aliyense amafuna chimwemwe chenicheni ndi chikhutiro cha mtima. Anthu ena amachisakasaka m’zinthu zakuthupi, m’nyumba zachifumu ndiponso m’magalimoto. Ena amazifufuza m’malo ochitirako tchuti, malo okopa alendo komanso m’malo ochitirako zamsangulutso. Ena amaufunafuna m’maseŵera ndi za nsangulutso.
Komabe, Allah wayika chisangalalo chenicheni ndi chikhutiro cha mtima mu chikondi ndi kukumbukira Kwake. Chikondi cha Allah ndiye gwero la chisangalalo chenicheni ndi kukhutitsidwa kwa mtima.
Mu Quraan Majiid Allah akuti:
آلَا بِذِكْرِ اللَّهِ تَطْمَئِنُّ الْقُلُوبُ الله
Zindikirani! Kudzera mukukumbukira Allah ndi m’mene mitima imapeza chisangalalo (ndi chimwemwe).
Munthu akamalingalira za munthu, amazindikira kuti Allah Wamulenga ndi miyeso iwiri. Choyamba ndi thupi lake lanyama lomwe lili ndi mawonekedwe akunja, ndipo lachiwiri ndi thupi lake lauzimu lomwe lili ndi mzimu wake (ruuh).
chifukwa cha thupi lamunthu, kenako Allah adalilenga kuchokera ku dothi. kotero, thupi limafunikira zinthu zakuthupi pano pa dziko lapansi monga (chakudya, chakumwa, zovala ndi zina zotero) zinthu zopatsa thanzi, kukhutitsidwa ndi kukhutira.
Komatu thupi lauzimu la munthu (Ruuh), ndiye popeza Allah sadalilenge kuchokera kunthaka, koma adalilenga kumwamba, chakudya chake ndi, kukwaniritsidwa kwake ndi kukhutitsidwa kwake kumapezeka kudzera muzochita za kumwamba.
Zochita zakumwambazi zikutanthauza malamulo a shari’ah (monga swalah, zakaat, kusala kudya, ndi zina zotero) zomwe zimakhala ngati chakudya chauzimu.
Munthu akaswali, kusala, kupereka swadaqah, kuwerenga Quraan Majiid ndikuchita ibaadah zina, ndiye kuti mzimu wake umalandira chakudya chauzimu chimene Allah adachilenga kukhala riziki lake ndi chakudya chake.
Choncho, mzimu wake (mtima wauzimu) umaunikiridwa ndi mfundo za shari’ah ndipo amaona chisangalalo ndi kukhutitsidwa.
M’malo mwake, munthu akachita zoipa ndi machimo monga kugwiritsa ntchito maso molakwika, kudya zinthu za haraam, kuba, kuchita zina, kupondereza anthu, kuchita zinthu mopanda manyazi, njuga, ndi zina zotero ndiye kuti mtima wake umataya dangalira la Imaan ndikukwiririka mumdima wa machimo.
Zotsatira zake amadzimva kuti ndi osowekera komanso opelewedwa ndipo mzimu wake umasowekera kukhutira ndi kukwanirtsidwa.
Njira Yopezera Kukhutira Kwa Mtima
Olungama kwambiri komanso wanzeru pa nthawiyo Olemekezeka Moulana Ashraf Ali Thanwi (Rahimahullah) adanenapo izi:
Kupeza chimwemwe chenicheni sikumachokera pa kukhala ndi chuma chambiri. M’malo mwake, kupeza chimwemwe chenicheni kwazikidwa pa kukhala ndi mtima okhutira. Kukhutitsidwa kwa mtima ndi mzimu uku kungapezeke pokwaniritsa malamulo a shari’ah ndi kulimbikitsa ubale wa munthu ndi Allah.
Ngati munthu akhala okhanzikika pa dini ndikukwaniritsa malamulo a shariah, ndiye kuti ngakhale alibe zambiri zapadziko lapansi, adzapeza chisangalalo chamumtima ndi kukhutira. M’malo mwake, ngati munthu sali olimba pa deen, ndiye kuti ngakhale ali ndi zochuluka kwambiri za pa dziko lapansi mtima wake udzakhala opanda chimwemwe chenicheni.