Ena mwa madaritso aukuluakulu a Mulungu pa munthu, ndi mdaritso okhala ndi makolo. Mwayi okhalandi makolo ndi mdaritso ofunika kwambiri ndipo ulibe mlowa m’malo komanso umaperekedwa kwa munthu kamodzi kokha m’moyo wake.
Monga momwe chisomo cha kukhala ndi moyo chimaperekedwa kamodzi kokha kwa munthu, ndipo chikatha sichidzabwereranso, momwemonso chisomo chokhala ndi makolo, chikachotsedwa, sichingabwezeretsedwenso.
Mtendere ulionse omwe munthu ali nawo uli ndi maufulu ena omwe ali nawo. Pamene Mwayi okhala ndi makolo uli mgulu la zabwino kwambiri, ndiye kuti maufulu omwe ali nawo ndi ena mwa maufulu ofunikira kwambiri mu chisilamu.
Quraan yolemekezeka ndi Mahadith ndi zodzadza ndi malamulo ndi malangizo okhudza kufunikira kwakukulu kokwaniritsa maufulu a makolo ndikuwachitira zabwino zochuluka.
Mu Quraan Majiid Allah Taala wanena kuti:
وَقَضَىٰ رَبُّكَ أَلَّا تَعْبُدُوا إِلَّا إِيَّاهُ وَبِالْوَالِدَيْنِ إِحْسَانًا ۚ إِمَّا يَبْلُغَنَّ عِندَكَ الْكِبَرَ أَحَدُهُمَا أَوْ كِلَاهُمَا فَلَا تَقُل لَّهُمَا أُفٍّ وَلَا تَنْهَرْهُمَا وَقُل لَّهُمَا قَوْلًا كَرِيمًا ﴿٢٣﴾
Mbuye wako walamula kuti musapembedze aliyense koma lye, ndi kuti muchitire zabwino makolo anu. Ngati mmodzi wa iwo kapena onse awiri akalamba, Usanene kwa iwo: “Uff (mawu achipongwe kapena mawu aukali kapena mkwiyo)”, Ndipo osawakalipira, ndipo uwalankhule ndi mawu aulemu. “
M’ Hadith zidanenedwa kuti Chisangalalo cha Allah Taala chili m’chisangalalo cha makolo, ndipo mkwiyo wa Allah Taala uli m’kuipidwa kwa makolo”
Makolo Anu ndi Jannah Yanu kapena Jahannum
Tsiku lina Swahaabi wina adafunsa kwa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) za ufulu wa makolo. Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Iwo (makolo) ndi Jannah yako kapena Jahannam yako.”
M’mawu ena, ngati wina ali wachifundo ndi wachikondi kwa makolo ake ndi kuwamvera mu zinthu zonse zoloredwa, adzadalitsidwa ndi Jannah. Koma ngati wawanyoza ndi kuwachitira nkhanza komanso mwano, ndiye kuti kuwazunza kwake ndi chifukwa choti adzalowe ku moto wa Jahannam.
Makomo awiri aku Jannah akhala otsegula
Mu Hadith ina Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati:
“Nsilamu aliyense angakhale tsiku linse makolo ake ali osangalatsidwa naye (amamumvera Allah kudzera mukukwaniritsa maufulu a maokolo) makomo awiri aku Jannah amakhala otsegula kuti aloweko, ngati kholo limodzi ndi lomwe liripo khomo limodzi lokha ndi lomwe limakhala lotseguridwa”
“Nsilamu wina aliyense amene tsiku lonse lingadutse makolo ake ali okhumudwa naye (sakumvera Allah kudzera mukusakwaniritsa maufulu a makolo) makomo awiri aku Jahannam akhala otsegula, ngati kholo limodzi lokha ndi lomwe liri moyo khomo limodzi lokha ndi lomwe limakhala lotseguridwa”
Nkhani ya munthu wina kuwabeleka mayi ake popanga Twawaaf
Zanenedwa kuti tsiku lina lake olemekwzeka Abdullah bin Umar (Radhwiyallahu anhu) ankapanga twawaaf pamene adaona munthu wina ochokera ku Yemen atabereka mayi ake kunsana popanga twawaaf.
Mayi akewa atawanyamura choncho ankatulutsa mayi a ndakatulo:
Ndiine ngamila yawo yomvera chokwera china chirichonse cjomwe angakwere chitha kuwaopseza, koma ibe sindidzawachitira choipa chirichonse (kutanthauza kuti sindidzawaobetsera nkhanza zirizonse) pa nthawi ino ndawabeleka kunsana kwanga, koma nthawi yomwe adandinyamula m’mimba mwawo idali yaitali.
Atamaliza kupanga Twawaaf munthuyo adamufunsa Abdullah bun Umar (Radhwiyallahu anhu) kuti: kodi ndakwaniritsa ufulu wa mayi anga pobeleka kunsana kwangapamene amapanga Twawaaf?
Olemekezeka Ibnu Umar adaynkha:
Ayi! Ndipo siunathe kuwalipira ka mphindi kochepa ka ululu umene adamva pa nthawi imene unkabadwa.
Kumvera ndi kutumikira makolo ndi njira yopitira ku Jannah. Kuonetsetsa kuti makolo akutakasuka, kukwaniritsa zosowa zawo komanso kuwalemekwza ndi ibaadah yaikulu kwambiri yomwe imapezetsa malipiro ochuluka pano padziko loapansi komanso umoyo umenw uli nkudza.
Malipiro a Haji yovomerezeka
Olemekezeka Abdullah bin Abbaas, Mulungu asangalale naye, akunena kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Palibe mwana omvera amene amawayang’ana makolo ake mwachifundo (ndi chikondi) koma kuti Allah amapeleka kwa iye malipiro a Haji yovomerezeka kwa nthawi iliyonse akayang’ana makolo ake mwachifundo.”
Ma Swahaabah Radhwiyallahu anhum adafunsa, “Ngakhale atawayang’a kakhumi tsiku lililonse?” Mtumiki (Swallallahu alaihi wasllam) adati: “Inde, Allah ndi wamkulu ndipo Ngwaukulu kwambiri (malipiro ake ndi ochuluka kuposa momwe mukuganizira).
Olemekezeka Haarithah bin Nu’maani Kuwayang’anira Mayi Ake
Olemekezeka Haarithah bin Nu’maani ndi Swahaabah m’modzi wachi Ansaari otchuka kwambiri yemwe adatenga nawo gawo kwambiri pa nkhondo ya Badr.
Pa zabwino zonse za Swahaabah ameneyu, chinthu chimodzi chomwe ndi chosilirika kwambiri ndi chikondi komanso ulemu umene ankaonetsa kwa mayi ake olemekezeka Ja’dah (radhwiyallahu anha) zomwe zidaonekera kwambiri.
Tsiku lina Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adafotokoza za maloto omwe adaona kuti analota ali ku Jannah komwe anamva mawu a munthu akuwerenga Quraan.
Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) anafunsa kuti ndindani munthu amene amawerenga Quraan, anamuyankha kuti munthu amene amawerenga Quraan adali Haarithah bin Nu’maan (radhwiyallahu anhu).
Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) Atamaliza kufotokoza kenako adawauza ma Swahaabah (radhwiyallahu anhum) kuti ulemelero wapamwamba umene olemekezeka Haarithah anali nawo ndi chifukwa chowamvera ndikuwatumikira makolo ake.
Zanenedwa kuti olemekezeka Haarithah radhwiyallahu anhu panafika pomadyetsa mayi ake ndi dzanja lake powamawaika chakudya mkamwa ndi dzanja lake.
Kuposera zimenezo, mayi ake akamuuza apange china chake ndiye sanawamvetse chifukwa chotsitsa mawu kwambiri Kamba kokalamba, m’malo mowabwerezetsa zimene ayankhula amafunsa anthu omwe ali pafupi ngati amva.
Linali khalidwe labwino limeneri lowasamalira amayi ake mwachikondi ndi ulemu lomwe lidamupezetsa ulemelero wapamwamba lomwe linachititsa kuti Mtumiki swallallahu alaihi wasallam mwini wake adamumva akuwerenga Quraan yolemekezeka.
Osapereka vuti kwa makolo
Ngati tingaipange mitima ya makolo athu kusangalala adzatipangira duwa yochokera pansi pa Mtima.
Pomwe mbali inayi ngati tingawakhumudwitse tidzapeza tchimo lalikulu ndiumanidwa zabwino,chimwemwe ndi madalitso moyo wathu onse.
Kupitiriza pamenepo zanenedwa kuti munthu amene angachitire mwano makolo ake adzalangidwa pano padziko lapansi kupatula pa chilango chomwe akalandire tsiku lachiweruzo.
Mtumikimadalitso ndi ntendere zipite kwa iye adati,Allah adzakhululuka tchimo lieilonse ngati atafuna kupatura tchimo losawamvera makolo (Allah samakhululuka cthimo limeneli pokhapokha utapepesa kwa makolo ako).
“Ndithudi Allah adzalanga munthu amene oteroyo pa dziko pomwe pano asadamwalire (kupatula chilango chomwe adamusungira umoyo omwe ukubwera chifukwa chowakhumudwitsa makolo ake, adzalangidwa padziko pano)”
Komabe ngati makoowo atamakulamura kuchita zinthu zosemphana ndi shariya adzafunika kuti apewe zinthu zoterozo chifukwa lamulo la Allah liyenera kukhala pa tsogolo.
Olemekezeka Abu Hurairah radhwiyallahu anhu Kutumikira Mayi Wake
Olemekezeka Abu Hurairah ndi Swahaabi m’modzi odziwikika mwa ma Swahaabah a Mtumiki wa Allah swallallahu alaihi wasallam. Adalowa Chisilamu m’chaka cha 7 A.H ndipo adakhala ndi Mtumiki swallallahu alaihi wasallam mpaka kumapeto kwa moyo wake. Ngakhale adakhala zaka zochepa chabe ndi Mtumiki swallallahu alayhi wasallam Allah adamdalitsa ndi ulemelero ofotokoza Mahadith ochuluka kuchokera kwa Mtumiki swallallahu alaihi wasallam
Abu Hurairah radhwiyallahu anhu nthawi zonse amakhala akutumikira amayi ake omwe anali okalamba ndipo ankamudalira. Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adamulamura kuti akhalebe mu khidmat ya mayi ake okalamba.
Zanenedwa kuti pankhondo ya Khaibar, Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adalankhula ndi ma Swahaabah ndikuwalimbikitsa zopita nawo ku jihaad. Atamva izi, ma Swahaabah nthawi yomweyo adachita changu kukonzekera jihaad.
Nayenso Abu Hurairah radhwiyallahu anhu adafunitsitsa kutenga nawo mbali pa kampeni ndi kukamenya nawo Jihaad kumbali ya Mtumiki swallallahu alaihi wasallam. Komabe, mayi ake ankafunikira thandizo lake ndi khidmah yake. Choncho adapita kwa mayi ake nati: “Chonde ndiloreni ndikonzekere ndikupita ku Jihaad, popeza Mtumiki swallallah alaihi wasallam wawalamura ma Swahaabah kuti akonzekere ndi kutuluka kuti akamenye jihaad.”
Mayi ake atamva izi sanasangalale ndipo anati, “Upita bwanji pamene ukudziwa mavuto omwe ndingakumane nawo iwe kulibe?” Koma chifukwa chofunitsitsa kugwirizana ndi Mtumiki, adanenetsa kuti: “Sindingathe kutsala m’mbuyo ndi kusiyana ndi Mtumiki swallallah alaihi wasallam.”
Amayi ake adapitilizabe kumudandaulira ndipo adamukumbutsanso za ufulu wake pa iye chifukwa chomulera komanso kumuyamwitsa kuyambira ali wakhanda, komabe adaonetsa kulimba mtima kufuna kupita nawo ndi gulu la Mtumiki swallallah alaihi wasallam.
Kotero mai ake a Abu Huraira adadza kwa Mtumiki swallallah alaihi wasallam mwachinsinsi ndikumuuza zomwe zidachitika. Iye anafotokoza kuti mwana wake anali ofunitsitsa kupita nawo ku Jihadi, koma iwo akufunikira khidmah kunyumba. Atamva madandaulo amayiyu, Rasulullah swallallah alaihi wasallam adati, “mukhozna kupita, ndipo vuto lanu likonzedwa.”
Pambuyo pake, Abu Hurairah radhwiyallahu anhu anabwera kwa Mtumiki swallallah alaihi wasallam ndipo Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adatembenukira kumbali, Abu Hurairah nthawi yomweyo adazindikira kuti Mtumiki (Swallallaahu ‘alaihi wasallam) waipidwa naye ndipo anati: “E, Mtumiki wa Allah (Swalla Allaahu ‘alaihi wasallam) ndikudziwa kuti mukunditembenukira kumbali ineyo, ndikudziwa kuti mwakhumudwa nane chifukwa cha dandaulo lomwe mwalandira lokhudza.”
Mtumiki swallallah alaihi wasallam adalankhula naye nati: “Kodi iwe ndiwe amene amayi ake akumchonderera mpaka kufika pomukumbutsa za haqq yawo pa iye chifukwa chomuyamwitsa? ukuganiza kuti siuli m’njira ya Allah? Koma munthu akawachitira zabwino makolo ake ndi kuwakwaniritsira maufulu awo ndiye kuti iye ali m’njira ya Allah
Choncho Abu Hurairah radhwiyallahu anhu adakhala kunyumba ndi mayi ake ndipo sadapite nawo paulendowu. M’malo mwake Abu Hurairah radhwiyallahu anhu adadzayankhula patsogolo pake kuti: kwa zaka ziwiri chichitikireni zimenezi kufikira pamene mayi anga adamwalira ndidakhala nawo limodzi kuwayang’anira ndipo sindidatenge nawo gawo pa Jihadi iliyonse.”
Kuchokera pa Hadith imeneyi tikuphunzirapo za malipiro ochuluka kwambiri omwe munthu angalandire chifukwa chowayang’anira bwino makolo ake.
Ma Ufulu 14 a Makolo
Olemekezeka Moulana Abraarul Haqq sahib rahimahullah analongosora ma ufulu okwana khumi ndi anayi okhudza makolo (asanu ndi awiri owaonetsera pamene ali moyo ndipo asanu ndi awiri owachitira atamwalira)
Ma ufulu 7 okhudza pamene ali moyo
1. Azmat: kuwalemekeza.
2. Muhabbat: kuwakonda ndi kuwaonetsera chikondi.
3. Itaa’at: kuwamvera.
4. Khidmat: kuwatumikira.
5. Fikr-re- Raahat: kuwakhanzika umoyo osangalala ndi ofewa.
6. Raf-e-Haajat: kuwapatsa chisamaliro chonse.
7. Kuwayendera pafupi pafupi.
Ma ufulu 7 Okhudza Pamene Atisiya
1. Dua-e-Maghfirat: kuwapemphera chikhululuko kwa Allah komanso chifundo.
2. Esaal-e-sawaab: kuwatumizira sawabu (powaperekera sadaqa, kupanga ma nafl osiyanasiyana ndi niyah yoti malipiro ake apite kwa iwo pafupi pafupi).
3. Ikraam-e-A’izzah wa Ahbaab: kuwalemekeza abale awo, anthu omwe ankacheza nawo ndi onse omwe ankagwirizana nawo.
4. I’aanat-e-A’izzah wa Ahbaab wa Ahl-e-Qaraabat: kuwathandiza abale awo, anzawo komanso oyandikana nawo mmene ungakwanitsire.
5. Adaa-e-Dain wa Amaanat: kubweza ngongole zonse zomwe anali nazo komanso katundu yense wa anthu yemwe ankasungitsidwa.
6. Tanfeez-e-Jaaiz Wasiyyat: kukwaniritsa wasiyyah omwe anasiya ngati ndi oloredwa.
7. Kukazonda manda awo.