Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 4

9. Pamene mukupanga dua, mtima wanu uyenera kukhala olunjika ndi kukhala ndi chidwi kwa Allah, Mtima wanu usakhale osalabadira komanso osaganizira pamene mukupanga dua. Musamamwaze maso kuwayang’ana anthu pamene mukupanga dua.

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Pemphani kwa Allah motsimikiza ndi mwachiyembekezo kuti duwa yanu yayankhidwa, ndipo kumbukirani kuti Allah sayankha duwa lochokera mu mtima osakhala ndi chidwi ndi osalabadira.”

10. Pemphani Zofuna zanu zonse Allah, zazikulu kapena zazing’ono.

Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu Alaihi Wasallam) adati: “Aliyense wa inu atembenukire kwa Mbuye wake, Allah pa chosowa chake kapena pa zosowa zake zonse (ofotokoza nkhaniyo adakaika ngati liwu la Hadith lidali chosowa chake kapena” pa zosowa zake zonse’), kotero kuti ayeneranso kupempha kwa Allah ngakhale chingwe cha nsapato yake chikaduka, kapenanso kum’pempha kuti amupatse mchere (akafuna mchere).

11. Musamapange dua mukakumana ndi zovuta pokha. M’malo mwake, Pangani dua nthawi zonse, kaya m’mavuto kapena m’tendere.

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu Alaihi Wasallam) adati: “Amene akufuna kuti Allah amuyankhe dua yake pa nthawi yamavuto ndi m’masautso ayenera kupempha mochuluka mu nthawi ya mtendere ndi chitonthozo.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 1

1. Yambani dua pomulemekeza Allah kenako mudzamuwerengera duruud Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Pambuyo pake, modzichepetsa …