Chikhulupiliro cha Umar (radhwiyallahu ‘anhu) mwa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adafika kumalire a Shaam (Syria) atauzidwa za mliri omwe udawagwera anthu a ku Syria.

Sayyiduna Umar (Radhiya Allaahu ‘anhu) adati: “Ngati imfa ingandifikire Abu ‘Ubaidah bin Jarraah (Radhiya Allaahu ‘anhu) akadali ndi moyo, ndiye kuti ndidzamuika kukhala Khalifa pambuyo panga, ndipo ngati Allah Ta’ala atafuna kundifunsa kuti, ‘Bwanji unamuika Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) kukhala khalifah kuti alamulire Asilamu (pambuyo pako)?” Ndidzamuuza Allah Ta’ala chifukwa chimene ndinamuika kuti ndikhale kuti ndidamumva kale Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) akunena kuti, “Nabi aliyense adali ndi omutsatira odalirika (ochokera mu ummah wake) ndipo otsatira wanga odalirika (mu ummah wanga) ndi Abu Ubaidah bin Jarraah (Radhiyallahu ‘anhu). (Musnad Ahmad #108)

Zanenedwa kuti Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) atatsala pang’ono kumwalira, adapanga gulu la ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) asanu ndi m’ modzi ndipo adawalangiza kuti asankhe pakati pawo munthu amene angakhale khalifah. Pa nthawi imeneyo Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) ananenanso kuti: “Abu Ubaidah akadakhala kuti ali moyo lero, ndithudi, ndikadamsankha kukhala Khalifa (wa Asilamu).

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …