6. Popanga dua, musagwiritse ntchito njira yokayikira. Mwachitsanzo, musanene kuti: “E Allah, ngati Mukufuna kundikwaniritsira zosowa zanga kwaniritsani;
Olemekezeka Abu Hurayrah (Radhwiyallahu anhu) adasimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam adati; popanga dua m’modzi wa inu asanene kuti Ndichitireni chifundo ngati Mukufuna, ndikhululukireni ngati Mukufuna ndi ndipatseni mariziki ngati mujufuna.’ m’malo mwake apemphe chifundo cha Allah ndi mtima onse (kuti Allah Amufikitsa zosoŵa zake. Asampemphe Mulungu kuti ampatse chisomo Chake ngati akufuna) chifukwa Allah Palibe angamukakamize monga wafuna. Iye (kuchita chilichonse).”
7. Yembekezerani kwathunthu chifundo cha Mulungu uku mukupempha. Pangani dua motsimikiza kuti dua yanu iyankhidwa.
Abu Hurairah ( Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati Pemphani kwa Allah ndi chikhulupiriro chakuti duwa yanu iyankhidwa, ndipo kumbukirani kuti Allah samayankha dua yosachokera pansi pa mtima kapena opanda kuikira chidwi.”
8. Mtima wanu ndi ziyembekezo zitembenukire Kwa Allah yekha. Musamayembekezere chinthu china kusiya Allah, usakhale ndi maganizo akuti kudzera mwa wina wake kapena china chake zosowa zanu zikwaniritsidwa.