Zizindikiro za Qiyaamah 1

Mma hadith odalitsika, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adalosera zizindikiro zomwe zidzachitike Qiyaamah isanafike. Adauchenjeza Ummah za mayesero ndi masautso osiyanasiyana omwe adzawapeze m’malo osiyanasiyana komanso pa nthawi zosiyanasiyana pa dziko lapansi. Adawasonyezanso njira ya chiongoko ndi chipulumutso ku fitnah.

Uku ndiye kukongora kosayerekezeka ndi kupambana kwa Dini ya Chisilamu kuti Allah Ta’ala sanangotumiza Mtumiki Wake (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kuti akhale chiongoko ku Ummah, koma kuti adamudalitsanso ndi mphamvu yodziwa za zomwe zidzachitike pa dziko lapansi Qiyaamah isanafike ndi cholinga choti chiphunzitso chake chidzagwirizane ndi mavuto a nyengo zonse.

Choncho, tikupeza mfundo zabwino kwambiri zomwe zalembedwa mmahaadith olemekezeka, zomwe zikufotokoza za masautso apano ndi a m’tsogolo omwe Ummah udzakumane nawo pambuyo pa kumwalira kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam). Ena mwa ma fitnawa muli zisonyezo zing’onozing’ono komanso zikuluzikulu za Qiyaamah.

Olemekezeka Amr bin Akhtab (Radhwiyallahu ‘anhu) akuti: “Nthawi ina, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adayimilira mumzikiti nayamba kutifotokozera zomwe zidzachitike Qiyaamah isanafike. Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adakwera pa mimbar kutha kwa Swalah ya Fajr ndipo adalankhula mpaka nthawi ya Swalaah ya Dhuhr. Atatha Swalah ya Dhuhr, adakweranso pa mimbar ndikupitiriza kulankhula mpaka Asr. Atamaliza Swalah ya Asr, adakweranso pa mimbar ndipo adayankhula mpaka kulowa kwa dzuwa. Pakusonkhana kumeneko pa tsikulo, adatidziwitsa zomwe zidzachitike mu Ummah mpaka tsiku la Qiyaamah. Choncho, mwa ife amene amakumbukira kwambiri (zomwe adatiphunzitsa mtumikizi) ndi omwe ali odziwa kwambiri zisonyezo za Qiyaamah.” (Sahiih Muslim #2892)

Mahadith okamba za Qiyaamah ndi ambiri. Zizindikiro zina zafotokozedwa momveka bwino mwatsatanetsatane, pamene zizindikiro zina zafotokozedwa mwachidule. Choncho, chizindikiro chilichonse chimene Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adachifotokoza mwatsatanetsatane chikaonekera pamaso pa Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) zinkakhala ngati kuti mau a Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) akwaniritsidwa pamaso pawo.

Ma Ulama adazigawa zisonyezo za Qiyaamah m’magulu awiri; zisonyezo zing’onozing’ono ndi zikuluzikulu. Kuchokera muzizindikiro zing’onozing’ono, chizindikiro choyamba kuonekera chinali kumwalira kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), pomwe chizindikiro chachikulu choyamba kuonekera ndicho kutuluka kwa Imam Mahdi (Radhwiyallahu ‘anhu) padziko lapansi.

Insha Allah, m’zigawo zotsatira, tikambirana za zisonyezo zing’onozing’ono ndi zikuluzikulu za Qiyaamah zomwe zalongosoredwa Mmahadith pamodzi ndi kufotokoza matanthauzo a haadith paliponse pamene pakufunika.