Umar (Radhiyallahu ‘anhu) atachoka ku Madina Munawwarah kupita ku Baitul Muqaddas kuti akagonjetse, adayima ku Syria kuti akakumane ndi ma Swahaabah omwe ankakhala kumeneko. MaSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) adadzakumana naye (Radhwiya Allahu ‘anhu) yemwe adali kukhala ku Syria ndi kulamulira Syria, adawafunsa: “Ali kuti m’bale wanga?” maSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhu) adafunsa: “Kodi mukunena ndani?” Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) anayankha, “Abu ‘Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu).”
MaSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) adamuuza kuti Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) afika posachedwa kudzakumana naye. Patapita nthawi, Abu “Ubaidah (Radhwiyallahu ‘arıhu) anafika atakwera ngamira.
Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) adakumana ndi Umar (Radhwiyallahu ‘anhu), Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adawonetsa chisangalalo chachikulu ndi chimwemwe ndipo nthawi yomweyo adamukumbatira. Pambuyo pake Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adapereka khutbah kwa maSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) ndi onse omwe analipo. (Hilyatul Awliyaa vol. 1, p. 146 and Kitaabuz Zuhd libnil Mubaarak (rahimahullah])
Nthawi imeneyo, maSwahaabah (Radhwiya Allaahu ‘anhum) adamuyitanira Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti abwere (akadye).
koma Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) sanamuyitanire Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kunyumba kwake popeza pa nthawiyo adalibe chilichonse choti angamukobzere Umar (Radhwiyallahu ‘anhu).
Chifukwa cha ubale wabwino umene Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adali nawo ndi iye, Olemekezeka Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adalankhula naye nati: “E, iwe Abu Ubaidahl (Kuchokera mwa ma Swahaabah) mtsogoleri aliyense wankhondo wandiitanira kunyumba kwake kupatula iweyo.” Abu Ubaidah (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adati kwa iye: “E, Amiirul Mu-miniin! Ngati mungabwere kunyumba kwanga, ndithudi mugwetsa misozi.”
Komabe, Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adafuna kukacheza kunyumba ya Swahaabi wamkuluyu, choncho, Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) anamuyitanira Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kunyumba kwake ngati mlendo wake.
Umar (Radhiya Allaahu ‘anhu) atalowa mnyumba mwake, adadabwa kuona kuti zinthu zomwe adali nazo zinali zidutswa zochepa chabe za mkate ouma, thumba lamadzi, lupanga, chishango, thumba lachishalo, ndi bulangeti lachishalo lomwe ankagwiritsanso ntchito ngati chofunda chake ndi mtsamiro akamagona usiku.
Olemekezeka Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) ataona izi anayamba kulira ndipo kenako anamukumbatira Abu Ubaidah (Radhwiya Allahu ‘anhu) nati: “Ndithu, iwe ndiwe m’bale wanga. Ndapeza kuti maswahabah onse dziko lapansi lidawasintha (pamlingo onena kuti adapezera zinthu zapadziko lapansi kuti apindule nazo) kupatula iweyo.” Abu Ubaidah (Radhwiya Allahu ‘anhu) adayankha nati: “Kodi sindinakuuze iwe Amiirul Muminiin kuti ukadzacheza kunyumba kwanga udzakhumudwa (chifukwa chosapeza chuma cha padziko lapansi m’menemo)?”
Malinga ndi nkhani ina, Umar (Radhiyallahu ‘anhu) adamuuza kuti: “Bwanji osasunga zina?
zinthu zapadziko lapansi kapena zinthu zoti mupindule nazo?”
Komabe Abu Ubaidah (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adayankha nati: “E, iwe Amiirul Muminiin!Ndi Zambiri izi zikukwanira kukhala katundu wanga wapadziko lapansi pano mpaka pomwe ndikafikire mmanda.”