Zizindikiro za Qiyaamah 2

Cholinga Choufotokozera Ummah Zizindikiro za Qiyaamah

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adaufotokozera Ummah za zisonyezo zing’onozing’ono ndi zikuluzikulu zomwe zidzaonekere Qiyaamah isanabwere. Zambiri mwa zizindikiro zing’onozing’ono zakhala zikuonekera kale m’zaka mazana ambiri zapitazo, pamene zambiri mwa zizindikirozi zikuchitiridwa umboni lerolino.

Aalim wina yemwenso ndi Muhaddith, Allaamah Qurtubi (rahimahullah), watchula zifukwa ziwiri zolinga zimene Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) anafotokozera zisonyezo za Qiyaamah ku Ummah:

(1) Ummah ukadzaona chizindikiro chilichonse, chidzakhala chikumbutso kwa iwo kuti udzuke ku tulo take ndi kunyalanyaza kwake ndi kubwelera pa Dini.

(2) Udzatha kudzipulumutsa ku ma fitnah a nthawiyo potembenukira kwa Allah Ta’ala kulapa ndi kukonzekera za tsiku lomaliza. (Ta’leeq-us-Sabeeh 7/176)

Zina mwa zizindikiro zing’onozing’ono zomwe zidachitika kale m’zaka zapitazi ndi izi:

1. Kugawanika kwa mwezi mnthawi ya Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam).

2. Kumwalira kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam).

3. Kuphedwa kwa olemekezeka Umar (Radhwiyallahu ‘anhu), Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi Ali (Radhwiyallahu ‘anhu).

4. Mliri wa Amwaas, mu ulamuliro wa Umar (Radhwiyallahu ‘anhu), momwenso anthu masauzande ambiri adamwalira.

5. Kugonjetsedwa kwa Baytul Muqaddas ndi kugwa kwa ufumu wa Rome ndi Persia komwe kunachitika mu ulamuliro wa Umar (Radhwiyallahu ‘anhu).

6. Kuphedwa kwa Husain (Radhwiyallahu ‘anhu) ku Karbalaa mu ulamuliro wa Yazeed bun Mu’aawiyah.

7. Kuphana komwe kudachitika ku Harrah (malo akunja kwa Madinah Munawwarah) komwe anthu masauzande ambiri, omwe mwa iwo anali maSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) ndi ma Taabi’een (Rahimahumullah), adaphedwa mwankhanza mu ulamuliro wa Yazeed bin Mu’aawiyah.

8. Ulamuliro wa Umar bin Abdul Aziz (Rahimahullah) ndi chilungamo chomwe chidali chochuluka padziko lapansi panthawiyo.

9. Kuukira kwa Tartar m’zaka za 700 AH kalendala ya Chisilamu.

10. Kugonjetsedwa kwa Istanbul m’manja mwa Muhammad Al-Faatih (Rahimahullah) m’zaka za 900 AH.

Chilichonse mwa zizindikiro zing’onozing’ono zomwe tazitchulazi zidaloseredwa ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) ndipo zidachitika chimodzimodzi monga momwe adanenera m’mahadith ake olemekezeka.

Mu Hadith yotsatirayi, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adatchulanso zisonyezo zina zing’onozing’ono za Qiyaamah. Ngati tingayang’anitsitse momwe ulili Ummah lero, tipeza kuti zambiri mwazizindikirozi zikuchitika padziko lonse lapansi. Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati:

“Pamene zolandidwa pankhondo zidzatengedwa ngati chuma cha anthu kuti chigawidwe pakati pawo, chuma cha anthu chikadzatengedwa ngati chuma cha wina aliyense, Zakaat ikadzatengedwa ngati msonkho, maphunziro a Dini akadzaphunziridwa ndi Zolinga zina osati kutukula Dini, mwamuna akadzamvera mkazi wake ndi kusamvera mayi wake, ndi kuliika bwenzi lake pafupi ndi iye, ndi kuwatalikira bambo ake, ndipo Mmizikiti mudzachuluka phokoso, ndipo munthu ochimwa moonetsera ku mtundu wa anthu adzakhala mtsogoleri wawo, ndipo munthu wapansi mwa anthu adzakhala nthumwi yawo, ndipo munthu adzalemekezedwa chifukwa choopa kuipa kwake, ndi atsikana oimba ndi zoimbira adzachuluka, ndipo vinyo adzamwedwa (poyera), Anthu omalizira a Umma uno adzawatemberera omwe adali mu Ummah uno, (zizindikiro izi zikadzaonekera) anthu adzayembekezere mphepo yamkuntho, zivomerezi, anthu kumira m’nthaka, kudzisintha nkhope zawo, kugwa kwa mvula ya miyala ndi zisonyezo zina zofananana nazo zomwe zidzatero. Zimenezi zidzachitika motsatizana monga momwe ngale za m’chingwe zimagwera motsatizanachingwe chikaduka.” (Sunan Tirmizi #2211)

Ziyenera kukumbukiridwa kuti Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adatumizidwa kukhala mtsogoleri wa anthu onse mpaka kumapeto kwa nthawi. Iye adalinso mtsogoleri wa Ambiyaa ndi ma Rasul (‘alaihimus salaam) onse akale. Choncho, pamene adalosera za kupezeka kwa zisonyezo zimenezi, cholinga chake chinali kuuchenjeza Ummah za mayesero amenewa, ndikuwasonyeza njira yachipulumutso pokumana ndi mayesero ndi zovuta zoterozo.

Allah Ta’ala aupulumutse Ummah kuti usagwere m’machimo onse ndi zoipa zonse ndikutikhanzika pa Chisilamu.