Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Ranılullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adakhala pamodzi ndi Abu Bakar (Radhwiyallahu ‘anhu), Umar (Radhwiyallahu ‘anhu), Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi maSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum). anapatsidwa chakumwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam),

Nabii Swallallah ‘alaihi wasallam) anatenga chakumwacho m’manja mwake ndikumupatsa Abu Ubaidah Radhwiyallahu ‘anhu) kuti amwe kaye. Komabe Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu, pofuna kumulemekeza Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), sadafune kumwa kaye ndipo adati kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam): “E, Mneneri wa Allah! Imwani kaye.”

Kenako Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati kwa iye: “Abu Ubaidah, yamba kumwa. Abu Ubaidah Radhwiyallahu ‘anhu) kenako adalandira chiwiyacho kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam).

Komabe, asanamwe, iye kachiwiri, chifukwa cha ulemu ndi chikondi kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), adati kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam): “E, Nabii wa Allah! tengani (ndi kumwa kaye). (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamuuza kuti:

اشرب فإن البركة مع أكابرنا

Abu Ubaidah yamba kumwa, mabarakah (madalitso) ali mwa akulu akulu athu ummah udzalandira madalitso ngati ungalemekeze akukuakulu powaika patsogolo pa zina zilizonse. Barakah yochokera kwa Allah yagona pa kuchitira ulemu akuluakulu awo ndi kuwalola iwo kuchita zinthu moyambilira)”

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adatchulapo.

من لم يرحم صغيرنا ويجل كبيرنا فليس منا

” Munthu amene sachitira chifundo achinyamata pakati pathu komanso osalemekeza akuluakulu pakati panu, ndiye kuti sali mwa ife. Satsatira njira yathu ya sunna).” (Majma’uz Zawaaid #8214)

N.B. Mukumbukire kuti munthu akamacheza ndi akuluakulu, sunna ndi kuwasonyezera chikondi ndi ulemu. Chizindikiro chosonyeza chikondi ndi ulemu kwa iwo n’chakuti munthu amawaika iwo patsogolo kuposa iye mwini.

Pachifukwa ichi pamene Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) imam wa ma Ambiya ndi Atumiki onse adapereka chakumwacho kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti amwe kaye, sadafune kuyamba kumwa , koma adapempha kawiri konse Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kuti amwe pambuyo pake popeza Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndi munthu amene anali oyenera kumwa kaye.

Komabe, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamulamula kuti amwe kaye, kotero kuti adagonjera, pomvera lamulo la Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) (kapena wamkulu wina aliyense) kudzaikidwa patsogolo kuposa chikhumbokhumbo chofuna kulemekeza iwo, ndipo izi zidzagwirizana ndi sunnah pankhaniyi.

Kuchokera mu nkhaniyi, tikuwona kuti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adafuna kuusonyeza Ummah udindo wapamwamba olemekezeka wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti nawonso amulemekeze moyenerera.

Njira imodzi yoti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) awaonetsere maswahabah (ndi Ummah) kulemwkezeka kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) inali kuwafotokozera ndi mawu. Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adachita izi poufotokozera Ummah kuti Abu Ubaidah Radhwiyallahu ‘anhu) ndi odalirika wapadera wa Ummah uwu,

Njira yachiwiri yoti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) awasonyezere maswahaabah (ndiponso Ummah) udindo olemekezeka wa Abu Uhaidah (Radhwiya Allahu ‘anhu) inali kuonetsera pamaso pawo zichitochito zomwe iwo angamvetse kufunikira ndi ulemelero wake. Choncho, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adaitanitsa chakumwa ndikumupatsa kuti amwe kaye Abu Ubaidah kuti awonetse Ummah udindo ndi ulemu wake.

Check Also

Kuopa Allah Taala

Qataadah (Rahimahullah) akusimba kuti Olemekezeka Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ankati, (chifukwa choopa kudzaima pamaso pa …