Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah m’munda wa zipatso wa Bani Saaidah) kuti asankhe khaleefa pakati pawo.

Nthawi imeneyo Abu Bakr ndi Umar anali m’nyumba ya Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) ndipo sankadziwa zomwe zinkachitika. Ali m’nyumbamo, Umar mwadzidzidzi adamva mawu kuitana kuchokera panja akunena, “Iwe mwana wa Khattaab! Tuluka ndikufuna kukambirana nawe chinachake)!” Komabe, Umar adayankha kuti, “Zipita popeza panopo ndatanganidwa kaye (panthawiyo, thupi lodalitsika la Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) lidali lidakali m’nyumba mwake ndipo linali lisanaikidwe m’manda)”

Kenako padatuluka mawu akuti: “Tulukani (chifukwa) chinthu chachikulu Chatsala pang’ono kuchitika. Ndipo ma Answaar asonkhana kuti adziikire okha mtsogoleri mwa iwo, choncho pitani kwa iwo nkhani isanafike povuta, komanso kusagwirizana kusanayambe pakati pa inu ndi iwowo.”

Atamva izi Abu Bakr ndi Umar (Radhwiyallahu ‘anhuma) nthawi yomweyo adachoka kunyumba ya Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) napita ku Saqeefah Banu Saaidah. Ali m’njira, anakumana ndi Abu Ubaidah bin Jarraah, yemwenso adatsagana nawo.

Atafika pa Saqeefah Bani Sa’eedah, kukangana kwa nthawi yayitali kudayamba pakati pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi ma Answaar. Abu Bakr (Radhwiya Allaahu ‘anhu adawafotokozera kuti adamva Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) akutchula kuti khaleefah atha kusankhidwa kuchokera ku ma Quraishi ndipo poti iwo sadali ma Quraishi, Khaleefa sangakhale ochokera mwa iwo. Abu Bakr (Radhwiya Allahu ‘anhu) adauza ma Answaar uku atagwira manja a Umar ndi Abu Ubaidah (Radhwiyullahu ‘anhuma) kuti: “Ndine okondwa kuti mwasankha aliyense mwa anthu khumiwa (kukhala khaleefah wa Asilamu, sankhani aliyense mwa iwo amene mwamfuna)”(Musnad Ahmad #191)

Pa nthawiyo Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adalankhula kwa Answaar nati: “E inu ma Answaar! Kodi simukudziwa kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adalamula Abu Bakr kuti awatsogolere anthu pa swalah? Ndindani mwa inu angalimbe mtima ndikuima kutsogolo kwa Abu Bakr (ndi kutsogolera Swalah ngati Khalifah)?” ma Answaar atamva izi adati: “Tikudzitchinjiriza kwa Allah kuti tiimirire pamaso pa Abu Bakr.

Pambuyo pake, Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adagwira dzanja la Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) nalonjeza kuti adzakhala okhulupirika kwa iye, kenako Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) kenako ma Ansaar ndi ma Swahaabah ena onse nawonso adalumbira kwa Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu)

Kuchokera apa, tikuona ulemelero waukulu wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu), kuti Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu) adanena kuti akhale khaleefah oyamba wa Chisilamu. Koma ma Swahaabah onse (Radhwiyallahu anhum), kuphatikizapo Abu Ubaidah (Radhwiyallahu anhu) sadavomereze pempholi, ndipo onse adavomereza kuti palibe Sahaabi yemwe ali wamkulu kuposa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo iye ndi oyenera kwambiri kutenga u khilaafat.

Check Also

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah …