Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 5

12. Mukamaliza dua yanu, nenani Aameen.

Abu Musabbih Al-Maqraaiy akusimba kuti: Nthawi ina tidakhala pansi ndi Abu Zuhair An-Numairi (Radhwiyallahu anhu) yemwe anali ochokera mwa ma Swahaabah (Radhwiyallahu anhu). Anali odziwa kulankhula. Aliyense mwa ife akamapempha ankati: “Tsindika duayo ndi mawu oti Aamiin, pakuti Amiin ili ngati chidindo papepala. Kenako anati: “Kodi ndisakuuzeni za izi? Usiku wina, tidatuluka ndi Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) ndipo tidapeza munthu yemwe ankachita dua mwamphamvu. Mtumiki (Swallallahu Alaihi Wasallam) adaima kuti amumvetsere ndipo adati, ‘Akatsindika dua yake, aipanga Jannah kukhala yotsimikizika kwa iye.’ Mwa m’modzi adafunsa kuti angatsindike bwanji dua yake? Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adayankha nati; azitsindika dua yake ndi mawu oti Aameen, Ngati angatsindike dua yake ndi Aameen, wapanga Jannah yake (kukhala yotsimikizika) munthu amene adamufunsa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adakamuuza munthu yemwe ankapanga dua uja kuti; oh uje ndi uje tsindika dua yako ndi mawu oti Aameen ndikulandira nkhani yosangalatsa yochokera kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam).

13. Mukamaliza dua yanu, werengani duruud shariif.

Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, “Dua imatsakamira m’malere pakati pa mitambo ndi dziko lapansi. Siimaka kumwamba ngati duruud ya Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) siinawerengedwe (palibe chitsimikizo cha kuyankhidwa). ”

14. Mukamaliza Duayi, yendetsani manja anu pankhope panu.

Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti nthawi zonse Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) akakweza manja ake kupanga duwa, sankawatsitsa kufikira atapukuta manja ake pankhope pake.”

15. Musamapemphe chilichonse choletsedwa kapena chosatheka (monga kukhala Nabi).

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Dua ya munthu idzalandiridwa nthawi zonse ngati sakupempha chinthu chochimwa kapena kudula ubale, komanso ngati sachita changu (mu dua yake). .” Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adafunsidwa: “Kodi munthu amafulumira bwanji? Mtumiki (Swallallahu alahi wasallam) anayankha kuti: “Munthu amanena kuti: ‘Ndachita dua ndipo ndapempha dua, koma sindikuona dua yanga ikuyankhidwa.’ Kenako amatopa ndikusiya kupempha.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 1

1. Yambani dua pomulemekeza Allah kenako mudzamuwerengera duruud Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Pambuyo pake, modzichepetsa …