Olemekezeka Talhah pa Nkhondo ya Uhud

Sayyiduna Zubair bun Awwaam Radhwiyallahu anhu ananena kuti pa nkhondo ya Uhud, Rasulullah swallallahu alaih wasallam adavala zovala zodzitetezera ziwiri mophatikiza.

Pankhondoyi, Rasulullah ankafuna kukwera pa thanthwe koma chifukwa cha kulemera kwa zovalazo adalephera kutero. Choncho adamupempha Talhah Radhwiyallahu anhu kuti akhale pansi kuti amuthandizire kuti akwere pa thanthwepo. Talhah Radhwiyallahu anhu nthawi yomweyo adakhala pansi ndikumuthandiza Rasulullah Swallallaahu alaih wasallam kukwera thanthwelo.

Olemekezeka Zubair Radhwiyallahu anhu akuti adamumva Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) akunena panthawiyo: “Yakhala waajib kwa Talhah (ie Jannah yasanduka waajib kwa Talhah).”

Pankhondo ya Uhud, Talha molimba mtima anatsagana ndi Mtumiki Swallallaahu alaih wasallam ndipo anamuteteza. Nthawi zonse Maswahaba akakambilana za nkhondo ya Uhud, ankanena kuti tsikuli (tsiku la Uhud) linali la Talha. Talhah adateteza Rasulullah Swallallahu alaihi wasallam ndi thupi lake. Adavulazidwa mabala opitirira makumi asanu ndi atatu pathupi lake, koma sadachoke kumbali ya Mtumiki Swallallaahu alaih wasallam, ngakhale kuti dzanja lake lidapuwala chifukwa cha mabala owopsa.

Check Also

Kuopa Allah Taala

Qataadah (Rahimahullah) akusimba kuti Olemekezeka Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ankati, (chifukwa choopa kudzaima pamaso pa …