Nthawi ina, Olemekezeka Talha (radhwiyallahu anhu) adalandira ndalama zokwana ma dirham zikwi mazana asanu ndi awiri kuchokera ku Hadhramaut. Kutada usiku, atagona, iye anasowa mtendere, kumangotembenuka kuchoka mbali Ina kupita uku.
Poona kukhumudwa kwake, mkazi wake adamufunsa, “Nchiyani chikukuvutitsani, iye adayankha “Kodi munthu angaganize bwanji za Rabb pomwe ali ndi chuma chochuluka mnyumba mwake? Ndikuopa kuti chumachi chikhala chiletso kwa ine, ndi kundichititsa kusakumbukira Allah ndikusamulabadira.
Mkazi wake olemekezeka adapereka maganizo akuti achigawe kwa ma Swahalah radhwiyallahu anhum a Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) atamva izi, Olemekezeka Talha radhwiyallahu anhu adakhanzikika mtima pansi nati: “Allah akuchitire chifundo! Mzimayi wabwino komanso olungama, mwana wa olungama” anali Umm Kulthum, mwana wamkazi wa Abu Bakr radhwiyallahu anhu
M’mawa mwake adachigawa chuma chonwe kwa ma Muhajiriin ndi ma Ansaar (Radhwiyallahu anhum). Mwa ma Swahaabah amene adawatumizira chumachi panali olemekezeka Ali radhwiyallahu anhu.
Mkazi wake atamuona akugawa chumachi kwa ma swahaabah adati kwa iye: “Kodi muli gawo lathu mu chuma ichi kuti tikwaniritse zosowa zathu?” Adamuuza iye kuti asunge chuma chotsala, chomwe chinali pafupifupi chikwi chimodzi cha ma dirham (Siyaru Aalamin Nuttals 3/24)