Zizindikiro za Qiyaamah 3

Zizindikiro Zing’onozing’ono kuchuluka Pambuyo pa Zizindikiro Zikuluzikulu

Ukawona zisonyezo zing’onozing’ono za Qiyaamah zomwe zidalembedwa Mmahaadith, munthu atha kuzindikira kuti ndi chiyambi cha kubwera kwa zisonyezo zikuluzikulu. Choncho, zoona zake ndi zoti, zizindikiro zing’onozing’ono zizidzaonjezereka pang’onopang’ono, mpaka pamapeto pake, zidzafika pachimake pa kubwera kwa zizindikiro zikuluzikulu.

M’mahadith ena, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alaihi wasallam) adalongosora kuchulukira kwa ma fitnah powafanizira ndi mdima wa usiku omwe umachuluka mumdima pamene usiku ukulowa. Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alaihi wasallam) adati: “Fulumirani kuchita zabwino  mafitnah omwe adzakhale ngati magawo a usiku asanayambike . Munthu adzakhala okhulupirira m’bandakucha ndi kukhala kafiri madzulo, kapena madzulo munthu adzakhala okhulupirira ndikukhala osakhulupirira pofika m’bandakucha. Adzakhala okonzeka kugulitsa Dini yake kuti akhale ndi chuma chochepa chapadziko lapansi. (Sahiih Muslim #118)

Zina mwa zinthu zomwe zidzasonkhezere kubwera kwa fitnah ndi kukonda chuma. Chifukwa cha chuma, anthu adzapereka zikhulupiliro zawo za Dini, kudzichepetsa ndi manyazi. Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati:

Qiyaamah ikadazandikira (mudzaona) anthu akupereka salaam kwa anthu odziwika okha, ndipo (mudzaona) mabizinesi akuyenda bwino mpaka kuti akazi azidzatuluka m’nyumba zawo kudzathandizira amuna awo pa malonda, ndi (mudzawaona) mabanja, maubwenzi akutha (chifukwa chokonda chuma) … (Musnad Ahmed #3870)

Ma Fitnah (Mayesero) Okwana Asanu Oopsya Kwambiri Amene Akusonkhanitsa Mitundu Ya Mayesero Onse

Zitakhala kuti ma fitnah onse amene atchuridwa m’mahadiith osiyanasiyana aunikidwe bwino bwino, akhonza kuikidwa mma gulu okwana asanu omwe angakhale oopsya kwambiri. Ma fitnah asanu amenewa ndi amene akusonkhanitsa China chilichonse konena kuti ndi amene ali tsinde lalikulu la cbionongeko cha deen ya munthu komanso amachititsa kuti munthu ayambe kuchita zoipa za mitundu ina kamba ka ma fitnah amenewa. Mayesero asanu oopsya wa ndi awa: (1)Kukonda kwambiri chuma komanso kutsata zilako lako za mtima. (2) Kutsatizira m’chitidwe wa u kafiri (uchikunja) komanso Ayuda (3)kusowekera kwa chiongoko (manyazi ndi kudzichepetsa) (4)kusowekera kwa kulemekeza Dini komanso kulemekeza ma ufulu a anthu ena.(5)Kukhutira ndi maganizo ako ndi kusatsatira Dini komanso kusakhala ndi anthu olungama ndi ma ‘Ulama a chilungamo.

Kutengera ma kuffaar komanso Ayuda

Pa mitundu ya mayesero asanu oopsya aja, mtundu oyambilira ndi kutengera chikhalidwe cha Akhristu ndi Ayuda. Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) analosera kuti mwa ma fitnah amene adzabwere qiyamah isanabwere, amene adzakhale chifukwa cha kuonongeka kwa umma uno ndi konena kuti ummah uno udzayamba kutsata ndi kudalira zochitika za anthu osakhulupirira.

Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati inu (ummah) mudzatsatira njira za anthu amene analipo inu musanabwere, pang’ono pang’ono komanso mofulumira mpakana kufikira poti atati iwo akalowe ku dzenje lomwe kuli ng’ona nanunso mudzatsatira. Maswahaba atamva zimenezi adafunsa kuti O Mtumiki wa Allah, kodi mukutanthauza ayuda ndi akhirisitu? Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adayankha kuti ndindaninso posakhala iwowo (amene ndikutanthauza). (Sahiih bukhaari#3456)

Mu Quraan komanso m’mahadiith anthu okhulupilira aletsedwa kukhala abwenzi a anthu osakhulupilila. Chifukwa chowaletsera anthu okhulupilira kukhala abwenzi a anthu osakhulupilila ndi chakuti anthu okhulupilirawo akhonza kuyamba kutsatira njira, mavalidwe, maonekedwe, zikharidwe ndinso zochita zawo zomwe zikhonza kupangitsa kuti tsopano ayambeno kunyalanyaza kapena kulekelera malamulo awo amene Allah anawalamura komanso asilamu anzawo. Nsilamu akangoyamba kuyedzamira mbali ya anthu osakhulupilira ndikuyamba kutsatizira zikhalidwe zawo, amayamba kukhala ngati omwewo ndikuyamba kulemekeza iwowo ndipo akhonza kuyamba kunyoza chikharidwe cha chisilamu ndi ulemelero wa chisilamu.

Kulowa Pansi Kwa Ulemelero Wa Chisilamu

Tsiku lina Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adawalankhula ma swahaba ndipo adawafotokozera zizindikilo zosiyana siyana za Qiyaamah. Titati tiunike mwachidwi zizindikiro zomwe Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adazifotokoza, tipeza kuti zikusonkhanitsa mitundu ya ma fitnah anayi omwe atchuridwa m’mwamba aja. Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati:

Pamene zopeza za ku nkhondo (Jihaad) zidzatengedwe kukhala ngati chuma cha munthu ndikumangochigawana pakati pawo, pamene katundu osungitsidwa adzatengedwe ngati ndi chuma chako, ndi pemene zakat idzakhale ngati chipsinjo, ndi pamene maphunziro a dini adzaphunziridwe ndi cholinga China posakhala cha dini, ndi pamene mamuna adzalemekeze mkazi wake ndi kunyoza mayi ake, ndi pamene munthu adzakonde make ndi kudana ndi bambo ake, ndi pamene maphokoso adzachuluke m’mizikiti, ndi pamene munthu ochita nsambi moonekera adzakhale mtsogoleri wa anthu, ndi pamene anthu onyozeka (apansi) adzakhale owaimilira anthu ena, ndi pamene munthu adzalemekezedwe chifukwa choopa zoipa zochokera kwa iye, ndi pamene atsikana oimba nyimbo komanso zida zoimbira nyimbo zidzakhale ponse ponse, ndi pamene mowa udzayambe kumwedwa poyera yera, ndi pamene anthu omalizira a ummah uno adzayambe kutembelera anthu oyambilila ( maswahaba, atsogoleri amene ali panjira yolondora komanso ma Ulama), (pamene nsambi zimenezi zidzaonekere), pamenepo ummah udzayembekezere chimpweya chotentha, zivomerezi, kumizidwa munthaka kwa anthu, kusintha kwa maonekedwe ankhope zawo, miyala yogwa ngati mvula kuchokera kumwamba ndi zilango zina zonga zimenezi zomwe zizidzagwa motsatizana ngati m’mene mikanda imalakatikira pansi kuchokera mu chingwe chikaduka. (Sunan Tirmizi #2211)

Njira Zomwe Ummah Ungapewere Ma Fitnah Amenewa.

Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adawalankhula maswahaba kuti pitirizani kuwalamura anthu kupanga zabwino ndi kuwaletsa kupanga zoipa kufikira pamene nthawi idzafike yomwe mudzaona kususukira chuma kudzatsatidwa (ndi anthu osusuka), zilakolako za mtima zidzatsatidwa, ndipo kupeza za dziko lapansi chidzakhala cholinga cha munthu posiya aakhirah, ndipo munthu adzakhala osangalatsidwa ndi maganizo ake. Pa nthawi imeneyo mudzakhale osamala kwambiri poziteteza nokha (kuchokera ku ma fitnah omwe adzakhale ponse ponse) ndi kusiya kusakanikirana ndi anthu. Popeza masiku amene adzabwerewo adzakhala masiku ofunika kupilira (maka maka kuteteza dini yako munthu kudzakhala kovuta). Pa nthawi imeneyo kugwiritsitsa malamulo a dini kudzakhala kowawa ngati m’mene kumawawira kufumbata khala la moto m’manja. Munthu amene adzakhale opanga ntchito za bwino munthawiyo azidzapeza malipiro a anthu okwana makumi asanu (50) amene agwira ntchito ya bwino ngati yomweyo. Pokumva zimenezi ma swahaba adafunsa. O Mtumiki wa Allah kodi malipiro a munthu oteroyo adzakhala ofanana ndi malipiro a anthu 50 ogwira ntchito munthawiyo? Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adayankha kuti ayi. Malipiro amenewa adzakhala ofanana ndi malipilro a anthu 50 ochokera mwa Iwo amene agwira ntchito zabwino. (ma swahaba). (Sunan Abu Dawood #4341)

Kuchokera mu hadiith imeneyi tikumvamo kuti mu nthawi yovuta yomwe ma fitnah adzakhale ponse ponse m’dziko, Njira yopewera ma fitnah amenewa umma uno ndiyo kugwiritsitsa mwa mphamvu din ndi kusiya kukhala malo pamodzi ndi anthu omwe awakhudza ma fitnah.

Tikuyenera kuzindikira kuti kuonjezereka kwa malipiro mpakana kufika pofanana ndi malipiro a ma swahaba, ndi chifundo chachikulu kwambiri cha Allaah Ta’ala pa ummah uno. Ma ulama amalongosora kuti kuonjezereka kwa malipiroku kwagona mu kachulukidwe osati maonekedwe. Izi ziri chonchi popeza kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati; atati wina wake mwa inu apeleke golide ochuluka ngati phiri la Uhud ngati swadaqa, siingafanane ndi mudd imodzi kapenanso theka la mudd ya njere yomwe swahaba m’modzi yekha adapeleka ngati swadaqa. (Sahiih ibnu Hibbaan #6994)