Kuolowa Manja kwa Olemekezeka Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu)

Ali bin Zayd (Rahimahullah) akusimba kuti nthawi ina yake, Nchikumbe wina adapita kwa Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti akapemphe thandizo kwa iye. Nchikumbeyu kudapezeka zoti adali m’bale wake wa Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo popereka pempho lake, adamupempha kudzera mu ubale omwe udalipo pakati pawo.

Talha (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adayankha: “Kupatula Inu, palibe amene adandipemphako thandizo kudzera mu ubale.” Kenako adati: “Ndiri ndi gawo la malo lomwe Uthmaan (Radhiyallahu ‘anhu) wanena kuti andigula pa ntengo wa ndalama zokwana madirhamu zikwi mazana atau (300,000). Mutha kutenga malowo. Ngati mungafune, ndigulitsa malowo kwa Uthmaan (Radhiya Allaahu ‘anhu) m’malo mwanu ndipo ndidzakupatsani ndalama zonse zimene ndingagulitsire.

Qabeesah bun Jaabir (Rahimahullah) adati: “Ndidakhala ndi Talha bin Ubaidillah (Radhiya Allahu ‘anhu) ndipo sindinapeze wina owolowa manja kuposa iye popereka chuma chambiri kwa osauka popanda iwo. kumupempha.”

Check Also

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah …