Tsiku lomwe sayyiduna Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallahu ‘anhu) adalowa Chisilamu, adayamba kuyitanira anthu ku Chisilamu, Allah Ta’ala adamupanga kukhala njira ya ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhun) ambiri kulowa Chisilamu. Mwa ma Swahaabah amene adalowa Chisilamu kudzera mwa Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu ‘anhu) anali Talhah bin Ubaidillah (radhwiyallahu ‘anhu).
Talhah (radhwiyallahu ‘anhu) akufotokoza kuti:
Tsiku lina ndinapita ku Busra kukachita malonda. Tsiku lina, ndinali pa msika wa Busraa pamene ndinamva m’busa wina akufuula kuchokera ku nyumba yake kuti, “Fufuzani ngati pali wina aliyense pano yemwe ndi wachokera ku Haram ya Makkah Mukarramah.” Ndidayankha kuti, “Ndine okhala ku Haram ya Makkah Mukarramah.”
Wansembe adafunsa: “Kodi Ahmad (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) waonekera kale?” Ndinamufunsa wansembe kuti andifotokozere bwino. “Mukunena ndani (dzina lake Ahmad)?” Adayankha wansembe. “Mwana wa Abdullah bin Abdil Muttalib. Uwu ndi mwezi omwe adzawonekere. Adzaonekere mu Haram ya Makka Mukarramah ndikusamukira kudera lamapiri la miyala) lomwe lili ndi kanjedza wambiri. Iye ndi omaliza mwa Ambiyaa (alaihimus salaam) musachedwe kumtsata iye.
Kukambitsina ndi wansembeyo kunakhudza kwambiri mtima wanga. Nthawi yomweyo ndinabwerera ku Makkah Mukarramah ndikuwafunsa anthu ngati pali china chatsopano chomwe chachitika ine kulibe kwa nthawi imene ndinali paulendo. Adayankha kuti: “Inde Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), odalirika wadzinenera uneneri, ndipo mwana wa Abu Quhaafah Abu Bakr (Radhwiyallahu “anhu) wagwirizana naye”.
Mosachedwetsa ndinapita kwa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) amene ananditengera kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alaihi wasallam) ndikulowa chisilamu komanso ndidamulongosolera Mtumiki tsatanetsatane wa zomwe zidachitika pakati pa ine ndi wansembe wa ku Busraa (Al-saabah 3/410-411).