Olemekezeka Talhah (Radhiyallahu ‘anhu) pa Nkhondo ya Uhud

Olemekezeka Jaabir bin Abdillah (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adati:

Pa tsiku la nkhkndo ya Uhud, pamene ma Swahaabah adayamba kuthawa kunkhondo, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adasiidwa yekha pamalo ena ndi ma Swahaaba khumi ndi awiri okha.)

Ma mushrikiin atapita kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) ndi ma Swahaabah khumi ndi awiri, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adatembenukira (kwa maswahaba khumi ndi awiriwo) nati: “Ndani mwa inu amene atapite kukamenyana ndi anthu awa?”

Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) adayankha: “Ndikamenyana nawo.”

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa iye: “Khala pano (ndi ine)”.

Kenako Sahaabi wina wachi Answaari adati: “Ndikamenyana nawo, Oh Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam).”

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa iye: “Pita.” Sahaabi ameneyu adamenya nkhondo mpaka adaphedwa.

Ma Mushrikiin adapitanso kachiwiri, kwa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adatembenukira kwa ma Swahaabah nafunsanso kachiwiri: “Ndani akamenyane ndi anthu awa ndi kutiteteza?”

Talha (Radhwiyallahu ‘anhu) adatinso: “Ndikamenyana nawo, Oh Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adatinso kwa iye: “Khala pano (ndi ine).”

Sahaahi winanso adati: “Ndikamenyana nawo, Oh Rasulu wa Allah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam).

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa iye: “Pita.” Sahaabi adamenya nkhondo mpaka nayenso adaphedwa.

Izi zidapitilira choncho, ndipo aliyense mwa ma Swahaabah khumi ndi awiriwo adapita patsogolo, kumenya nkhondo ndi kufera Dini, mpaka adangotsala Rasulullllah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) ndi Talhah ibn Ubaydillah (Radhwiyallahu ‘anhu).

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adatinso: “Ndani angakamenyane ndi anthu awa (ndikutiteteza)?”

Talha (Radhwiyallahu ‘anhu) adati: “Ndipita kukamenyana nawo.”

Kenako Talhah (Radhwiyallahu anhu) adapita kutsogolo ndikukamenya nkhondo ndi molimba mtima, kulimba mtima ndi mphamvu za Sahaabah khumi ndi mmodzi yemwe adali patsogolo pake mpaka dzanja lake linadulidwa ndi adaniwo, ndipo zala zake zidadulidwa. Panthawiyi, adawonetsa ululu wake ndipo adati, “Hissl”

Zitatha izi, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa iye: “Ukadakhala kuti udatchula dzina la Allah (panthawi imeneyo), Angelo akadakunyamula pakati pa anthu uku akukuyang’ana. “

Check Also

Olemekezeka Talhah pa Nkhondo ya Uhud

Sayyiduna Zubair bun Awwaam Radhwiyallahu anhu ananena kuti pa nkhondo ya Uhud, Rasulullah swallallahu alaih …