Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 6

16.Lekani kulongosora mwatsatanetsatane pa dua yanu. M’malo mwake, muyenera kupempha zabwino zonse.

Nthawi ina Abdullah bin Mughaffal Radhwiyallahu anhu anamva mwana wake akupempha m’mawu otsatirawa: “O Allah! Ndikukupemphani nyumba yachifumu yoyera kumbali yakumanja kwa Jannah ndikalowa m’menemo.” Atamva izi Abdullah bin Mughaffal (Radhwiyallahu anhu) adati: “E, mwana wanga! Mpemphe Allah Jannah, ndipo pempha chitetezo Chake kumoto wa Jahannum, monga m’mene ndinamumvera Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) akunena kuti: Pali gulu la anthu mu Ummah uwu lomwe lidzapyole malire pa twahaarah (monga wudhu, ghusl, ndi zina zotero). ndi kupanga dua.”

ادْعُوا رَبَّكُمْ تَضَرُّعًا وَخُفْيَةً ۚ إِنَّهُ لَا يُحِبُّ الْمُعْتَدِينَ ‎﴿٥٥﴾

Itanani Mbuye wanu modzichepetsa ndi mofewa, pakuti Allah  Sakonda amene amapyola malire.

17.Ndibwino kupanga dua yokwanira.

Bibi Aaishah (Radhwiyallahu anha) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) ankakonda ma duwa yomwe ya matanthauzo ochuluka, ndipo ankasiya ma dua enawo.

Awa ndi ena mwa ma masnuun dua omwe akufotokozedwa mu Hadith kuti:

رَبَّنَا آتِنَا فِي الدُّنْيَا حَسَنَةً وَفِي الْآخِرَةِ حَسَنَةً وَقِنَا عَذَابَ النَّارِ ‎﴿٢٠١﴾

E, Mbuye wanga, tipatseni zabwino padziko lino lapansi ndi tsiku lomaliza, ndipo tipulumutseni kumoto wa Jahannum.

اَللّٰهُمَّ إِنِّيْ أَسْأَلُكَ مِنْ خَيْرِ مَا سَأَلَكَ مِنْهُ نَبِيُّكَ مُحَمَّدٌ صَلّٰى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ وَأَعُوْذُ بِكَ مِنْ شَرِّ مَا اسْتَعَاذَ مِنْهُ نَبِيُّكَ مُحَمَّدٌ صَلّٰى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ وَأَنْتَ الْمُسْتَعَانُ وَعَلَيْكَ الْبَلَاغُ وَلَا حَوْلَ وَلَا قُوَّةَ إِلَّا بِاللهِ

Ee Allah  Ndikukupemphani zabwino zomwe Mtumiki Wanu, Muhammad (Swalla Allaahu ´alayhi wasallam) adakupemphani, ndipo  ndikudziteteza ku zoipa zomwe Mtumiki Wanu  Muhammad (Swallallahu alaihi wasallam) adakupemphani chitetezo. Kwa Inu nokha mukupemphedwa chithandizo, ndipo Inu nokha Mungathe kukwaniritsa chosowacho, ndipo palibe mphamvu (yopewa zoipa) ngakhale mphamvu iliyonse (Yochita zabwino) koma ndi chithandizo cha Allah.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …