Olemekezeka Talhah (Radhwiyallaahu ‘anhu) akuti:
Ma Swahaabah (Radhwiya Allahu ‘anhum) adauza munthu wina okhala kumudzi kuti: “Pita ukafunse kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) kuti Allah Ta’ala akunena za ndani (m’ndime yotsatira ya Quraan Majeed)” (ma Sahaabah) ndi amene adakwaniritsa lonjezo lawo (ndi Allah Ta’ala lokhala okhazikika pankhondo okonzeka kupereka moyo waowo ngati nsembe).”
Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) ankakanika kumudunsa (Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) mwachindunji) chifukwa cha ulemu waukulu omwe adali nawo kwa iye. (Choncho adampempha sahabayo kuti awadunsire kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) m’malo mwawo).
Swahabayu atamufunsa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) sadayankhe. Swahabayu adafunsanso kachiwiri ndi kachitatu, koma Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adakhala chete.
Olemekezeka Talhah (Radhwiya Allaahu ‘anhu) akuti:
Kenako ndinalowa mu Masjid nditavala kurta yobiriwira. Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) atandiwona, adati: “Ali kuti munthu amene amafunsa uja (Aayah yomwe Allah Ta’ala watchulamo) amene adakwaniritsa lonjezo lawo (ndi Allah Ta’ala) malo omenyera nkhondo ndi okonzeka kupereka miyoyo yawo chifukwa cha dini)”?”
Swahabayo adayankha nati: “Ine ndi amene ndimafunsa, Oh Mtumiki wa Allah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam).
Kenako Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Munthu akunenedwayu (akunena za Talhah (radhwiyallahu ‘anhu)) ali m’gulu la anthu amene adakwaniritsa lonjezo lawo (ndi Allah Ta’ala wokhanzikika pankhondo okonzekera kupereka miyoyo yawo chifukwa cha Dini awo).”