Mzake wa Nabi Musah ‘Alaihis Salaam ku Jannah

M’chisilamu ntchito iliyonse yabwino ili ndi kuthekera kolumikizitsa munthu ndi Allah ndikumupezetsa sawabu ku umoyo omwe uli nkudza, komabe pali ntchito zina zimene ndi zapederadera pamanso pa Allah ndipo zimatha kukhala njira yopezera ubwino wa Dini yonse ndi ubwino wa dunya pamodzi.

Zina mwa ntchito zimenezo ndi kuonetsa kukoma mtima ku zolengedwa za Allah ndikukhala okhudzika pa nkhani ya umoyo wake ndi Dini yake.

Pali nkhani zosiyanasiyana mu mbiri ya chisilamu zomwe zimaonetsa m’mene Allah adawaonetsera anthu chisomo chapadera ndikuwasintha miyoyo yawo kuchoka ku kukhala oipa ndikusanduka kukhala abwino chifukwa chochitira chifundo zolengedwa zake kaya ndi Asilamu, osakhulupirira ngakhalenso nyama.

M’munsimu muli nkhani yokhudza munthu amene m’maonekedwe ankaoneka kuti ndi munthu wamba, koma adapeza ulemelero wapamwamba ku umoyo winawo chifukwa chotumikira makolo ake ndi kukwaniritsa maufulu awo mwachikondi, chisoni ndi chifundo.

Dua yomwe adapeza kuchokera pansi pa mtima wa makolo ake idamupanga kukhala opambana kwambiri pamaso pa Allah kotero kuti adakhala bwenzi la Nabii Musah (mtendere ukhale pa iye) ku Jannah.

Zanenedwa kuti nthawi ina Nabii Musa, mtendere ukhale pa iye, adapempha kwa Allah, nati: “E, Allah ndionetseni mnzanga ku Jannah! Allah adayankha duwa ya Nabii Musah ‘alaihis salaam, adamuonetsa munthu wina ndipo adati: “E, iwe Musa, pita kumzinda wakuti-wakuti, chifukwa kumeneko ndi kumene ukampeze munthuyu amene ndi nzako ku Jannah.”

Choncho Nabiy Musa ‘alaihis salaam adanyamuka nayenda mpaka adakafika kumzinda umene Allah adautchura. Atafika mumzindawo, Nabii Musa ‘alaihis salaam, anakumana ndi mnyamata wina yemwe Allah adamuonetsa. Mnyamatayo anakumana ndi Nabii Musah ‘alaihis salaam ndipo anamulonjera, koma osadziwa kuti uyu ndi Nabii Musah ‘alaihis salaam Mneneri wa Allah.

Nabii Musah ‘alaihis salaam, adayankha moni wake, ndipo adamupempha mnyamatayo ngati iye angamulore kugona kunyumba kwake ngati mlendo wake.

Mnyamatayo anavomera nati, “Ndine okondwa kukulandirani ngati mlendo wanga. Ngati mungasangalatsidwe ndi chilichonse chimene ndikupatseni kuti mudye, ndiye kuti ndine okondwa kukusangalatsani ndi kukulemekezani.” Nabiy Musah ‘alaihis salaam, adayankha, “Ndine okondwa ndi chilichonse chomwe mungandipatse.”

Mnyamatayo anali ogulitsa nyama. Choncho, atamuvomera Nabii Musah ‘alaihis salaam monga mlendo wake, adapita naye kumalo ophera nyama ndipo adamupempha kuti adikire mpaka amalize ntchito yake ya tsikulo.

Nabii Musah ‘alaihis salaam akudikirira m’sitolo ya mnyamatayo, ankaona kuti mnyamatayo akapeza mafuta alionse kapena mafuta a m’mafupa, amawaika pambali n’kusunga.

Pamapeto pake, mnyamatayo atamaliza ntchito yake ya tsikulo, adamutengera Nabii Musa ‘alaihis salaam kunyumba kwake. Atalowa m’nyumba mwake, anatulutsa mafuta amene anasunga aja ndikuphika.

Atamaliza kudya analowa m’chipinda chimodzi cha m’nyumba mwake. Nabi Musah ‘alaihis salaam adaona kuti m’chipindachi munali madengu awiri akuluakulu (ofanana ndi nyundo) ataimikidwa pafupi ndi denga. Mnyamatayo anapita pa dengu lina, ndipo mosamala kwambiri ndi modekha, analitsitsa pansi.

Pamene ankatsitsa dengulo, Nabii Musah ‘alaihis salaam anaona kuti mkati mwake munali bambo ake a mnyamatayo amene anali atakalamba kwambiri. Mnyamatayo anatulutsa abambo akewo m’basiketiyo nawatsuka kumaso. Kenako anachapa zovala zake ndi kuzinunkhiritsa, kenako anawaveka abambo ake zovala zoyera ndi zonunkhira.

Atatero, anatenga mkate, naunyemanyema, nathirapo mafuta ophika. Kenako anapatsa bambo akewo madziwo mpaka anakhuta, ndipo kenako anawamwetsa madzi akumwa mpaka pomwe linathera ludzu.

Atatsiriza kuisamalira nkhalambayo motere ndi kukwaniritsa zofunika zake, nkhalambayo idamupemphera duwa kuti: “E mwana wanga! Allah asaipangitse ntchito yako yondisamalira kupita pachabe. Komanso Akuchite kukhala bwenzi la Nabiy Musa bin Imraan ‘alaihis salaam ku Jannah!

Kenako mnyamatayo anatsitsa basiketi yachiwiri ija, ndipo Nabii Musah ‘alaihis salaam anaona kuti m’kati mwake munali mayi ake a mnyamatayo amenenso anali atakalamba kwambiri. Mnyamatayo anawasamalira monga momwe anasamalirira abambo ake aja.

Pambuyo pomutumikira ndi kuona zosoweka zawo, adamupangira duwa kuti: “Alhamdulillah! E, mwana wanga! Allah Asaononge khama lako pakundisamalira, ndipo Akuchite kukhala bwenzi la Nabii Musah bin Imraan ‘alaihis salaam ku Jannah!

Nabii Musah ‘alaihis salaam ataona kukula kwa chifundo ndi chisamaliro chimene mnyamatayo anasonyeza kwa makolo ake okalamba, iye anagwidwa ndi chifundo ndi iwo. Motero, anayamba kulira, ndipo mkatikati mwake, anachoka panyumba ya mnyamatayo.

Ataona kuti Nabii Musah ‘alaihis salaam akunyamuka, mnyamatayo nthawi yomweyo adamutsatira popeza adali mlendo wake, adamupatsa zakudya zomwe adakonza.

Koma Nabiy Musah ‘alaihis salaam adati kwa iye: “E, m’bale wanga! Sindikufuna chakudya chako, chifukwa chomwe ndinabwelera kwa iwe ndikuti Allah ndimapempha kwa Allah kuti andionetse munthu yemwe atakakhale bwenzi langa ku Jannah ndipo wandiwonetsa kuti iwe ndiwe amene udzakhale bwenzi langa ku Jannah.”

Mnyamatayo adafunsa Nabii Musah ‘alaihis salaam Allah akuchitireni chifundo! Ndiuzeni ndiinu ndani?” Nabii Musah ‘alaihis salaam anayankha kuti: “Ndiine Nabii Musah bin Imraan.” Mnyamatayo atamva zimenezi anadabwa kwambiri moti anagwa pansi n’kukomoka.

Atatsitsimuka ndikudzuka, mnyamatayo adalowa mnyumba mwake ndikuwuza makolo ake nkhani yabwino yoti Allah wavomera dua yawo kuti akhale mnzake wa Nabii Musa ‘alaihis salaam ku Jannah.

Adawauza kuti munthu amene adali nayeyo siali wina koma Nabiy Musah ‘alaihis salaam iye mwini, ndipo adamfikitsira nkhaniyo kuchokera kwa Allah Mwiniwake kuti Allah wawavomera pempho lawo.

Makolowo atamva uthenga wabwinowu, anasangalala kwambiri moti anatulutsa mawu achimwemwe ndikumamwalira. Ghusl itatha, Nabiy Musah ‘alaihis salaam adaswalira swalatul Janaazah. Pambuyo pake, m’nyamatayo adatengana ndi Nabi Musah ‘alaihis salaam ndipo anakhala limodzi mpaka kumapeto kwa moyo wake.

M’nkhaniyi, tikuwona kuti chifukwa chimene m’nyamatayu adadalitsidwira kukhala bwenzi la Nabii Musah ‘alaihis salaam ku Jannah ndi chifukwa chakuti makolo ake adamuchitira maduwa ochokera pansi pa mtima chifukwa chowatumikira, kuwamvera ndi kuwachitira zabwino, chikondi ndi chifundo.

Check Also

Kodi Amaanah Imatanthauza Chiyani?

Amaanah imatanthauza kuti munthu akhale olingalira za tsiku lachiweruzo pamene adzaime pamaso pa Allah pankhani …