18. Popempha mpempheni Mulungu kuti akudalitseni ndi aafiyah (ie kuti akudalitseni momasuka m’magawo onse a moyo wanu).
Abbaas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti: “Nthawi ina ndinamufunsa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam): “E, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) wa Allah, ndiphunzitse duwa (yaphindu) imene ndiyenera kupempha kwa Allah. Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anayankha, “Pemphani kwa Allah kuti akudalitseni ndi Aafiyah (kumasuka kwakuthupi ndi kwauzimu).” Pambuyo pa masiku angapo, ndinadzanso kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) ndipo ndinamufunsa kuti, “E, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) wa Allah ndiphunzitse dua (yaphindu) imene ndiyenera kuipempha kwa Allah. Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anayankha kuti, “E, iwe Abbaas, iwe malume a Mtumiki wa Allah, pempha Allah kuti akudalitseni ndi aafiyah pa dziko lapansi ndi Aakhirah.”[1]
19. Lekani kudya zinthu zaharamu kapena chakudya chokayikitsa ndikuchita machimo. Kudya haramu ndikuchita machimo kumalepheretsa ma dua kuyankhidwa.
Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “E inu anthu! Allah walamula Asilamu ndi lamulo lomwe adawapatsa Ambiyaa . (Pankhani ya Ambiyaa(alaihimus salaam), Allah wati: “E inu Atumiki, idyani choyera ndi chabwino, ndipo chitani zinthu zabwino. Ndithudi, ine ndikudziwa zonse zimene mukuchita.” (Kwa okhulupirira) Allah wanena kuti: “E inu okhulupirira, idyani zakudya zoyera ndi zabwino zomwe takupatsani. Pambuyo pake, Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adalongosola za chikhalidwe cha munthu amene akuyenda ulendo wautali otopetsa. Tsitsi lake losapesa ndipo zovala zake zakuda ndi fumbi. Amakweza manja ake kumwamba, akulira mopempha nati: “E, Mbuye wanga! Komabe, chakudya chake ndi zakumwa zake ndi zaharaam, zobvala zake zachokera ku Haramu, ndipo thupi lake ladyetsedwa ndi haraam, ndiye ma dua ake angayankhidwe bwanji?” (i.e. Ngakhale ali m’masautso ndi maonekedwe omvetsa chisoni, ma dua ake sangayankhidwe).[2]
[1] سنن الترمذي، الرقم: 3514، وقال: هذا حديث صحيح
[2] صحيح مسلم، الرقم: 1015