Ubwino Osiya Pambuyo Mwana Olungama

Bambo a Nabii Yunus (alayhis salaam) adali munthu Owopa Allah dzina lawo Mattaa.

Iwo ndi mkazi wawo kwa nthawi yaitali ankafuna kuti Allah atawadalitsa ndi mwana wamwamuna ndi kumuchita kukhala Mneneri kwa Bani Israeil.

Zaka zambiri zidadutsa uku akumapempha mpaka pamapeto pake adaganiza zopita kukasupe odalitsika wa Nabii Ayyoob komwe adasambamo ndipo adapatsidwa shifaa (machiritso) yokwanira ndi Allah.

Onse awiri anapita kuchitsime ndikukasamba m’madzi ake. Kenako adaswali ndipo adamupempha Allah mu dua kuti awapatse mwana odalitsika yemwe adzakhale Nneneri kwa Bani Israeil.

Allah Taala adavomera dua yawo ndipo pambuyo pake mkazi wa Mattaa adatenga pakati pa Nabiy Yunus.

Patatha miyezi inayi ya pathupi, mwana adakali m’mimba, Mattaa anamwalira ndipo anasiyana nalo dziko lino.”

Ngakhale Mattaa sanakhale ndi moyo kuti aone chipatso cha dua yake, adasiya mwana yemwe adali opembedza ngati cholowa chake chomwe chidzapitirize kumpezera mphoto zazikulu pa Tsiku Lomaliza.

Cholowa Cha Tsiku Lachiweruzo

Kuchokera pa nkhani imeneyi, tikumvetsetsa kuti cholowa chachikulu kwambiri ndi kukhala ndi ana olungama. Cholowa chimenechi ndichoti sichidzathandiza munthu padziko lapansi, koma ubwino wake udzapitirira mpaka Tsiku Lachiweruzo.

Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati:

“Munthu akamwalira, ntchito zake zonse zimatha kupatula zinthu zitatu; sadaqah-e-jaariyah (ntchito zake zabwino zomwe malipiro ake ndi opitirira ngakhale iye itamupeza imfa), maphunziro ake omwe anthu amapindura nawo (iye atamwalira ndi mwana owopa Mulungu amene adzamupemphere Dua.”

Nkhawa ndi Dua ya Ambiyaa ‘alaihimus salaam pa ana awo

Munthu akaulingalira moyo wa Ambiya (Atumiki a Allah) ‘alaihimus salaam, ma Swahaabah Mulungu asangalale nawo, ndi owopa Allah kalero, adzapeza kuti adapanga dua yapadera pa ana oopa Mulungu amene adzakhale cholowa kwa iwo akadzamwalira.

Chimodzimodzinso, iwo ankakhala okhudzidwa ndi kupita patsogolo kwa Dini ya ana awo m’moyo wawo onse.

Choncho, Quraan Majiid ikutchura mwapadera za dua ya Nabi Ibraahim ‘alaihis salaam ndi Zakariya ‘alaihis saaam, yokhudza ana oopa Allah.

Chimodzimodzinso, pamene Nabi Ya’quub ‘alaihis salaam adali chigonere nthawi ya imfa yake, adalangiza ana ake kuti akhale okhanzikika pa Dini ngakhale iye akamwalira. Nkhaŵa yake yaikulu ngakhale pamene ankayandikira mapeto ake, inali chitetezo cha Dini ya ana ake m’mbuyo muno.

Nkhawa za maSwahaabah (Radhwiya-Alkahu anhum) kwa Ana awo

Mtumiki (Swallallahu alaikhi wasallam) atapanga Hijrah kupita ku Madina, Sayyiduna Ummu Sulaim (Radhwiyallahu anha) adabweretsa mwana wake wamwamuna Anas (Radhwiyallahuanhu) ndipo adamupempha kuti amulandire mwana wake kuti amutumikire.

Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) anali ndi zaka pafupifupi khumi panthawiyo. Adakhalabe akutumikira Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) kwa zaka khumi mpaka pomwe adamwalilira Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam).

Mosakayikira, kudali kukhudzika pa dini ndi kuleredwa kwa mwana wake ndi zimene zidamupangitsa kuti amutengere kwa Mtumiki (Swallallaahu alaihiwasallam) ndikumupereka pa ntchito yotumikira iye.

Momwemonso Abbaas (Radhwiyallahuanhu) adamulangiza mwana wake Abdullah bin Abbaas (Radhwiyallahuanhma) kuti akakhale ndi Mtumiki (Swallallaahu alaihiwasallam) kunyumba ya azakhali ake Bibi Maimuunah (Radhwiyallahuanha) kuti apindule ndi Swalah yake ya Tahajju ndi kupindula kudzera mukukhala naye.

Sayyiduna Abdullah bin Abbaas anali ndi pafupifupi zaka khumi ndi ziwiri kapena khumi ndi zitatu panthawiyo.

Ndi khumbo la kholo lililonse kuti mwana wake akhale otetezeka pambuyo pa imfa yake. Chifukwa chake, njira zofunikira zimaikidwa kuti ateteze tsogolo lazachuma la mwanayo.

Komabe, nkhawa yaikulu ya kholo iyenera kukhala chitetezo cha dini ya mwanayo, chifukwa ichi ndi chinthu chokhacho chomwe chingamuthandize kukhala olumikizana ndi Allah Wamphamvu yonse ndi kumupangitsa kukhala opambana padziko lapansi ndi lotsatira.

Check Also

Kufunikira Koti Mwana Adzicheza Ndi Anthu Abwino

Mu kulera mwana, ndi zofunika kwambiri kuti makolo azionetsetsa kuti mwana wawo nthawi zonse apezeka …