Olemekezeka Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu pa Nkhondo ya Uhud

Pankhani ya kupirira kwa Talha (Radhwiyallahu ‘anhu) pankhondo ya Uhud, Sa’d bin Abi Waqqaas (Radhwiyallahu ‘anhu) adanena izi:

Allah Ta’ala amuchitire chifundo Talha. Mosakayikira, mwa ife tonse, adamuthandiza kwambiri Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa wasallam) pa tsiku la Uhud.

Kenako Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adafunsidwa: “Tifotokozere momwe (adamuthandizira kwambiri Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)) E Abu Ishaq?”

Adanenanso kuti: “Iye adakhanzikika kumbali ya Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) pomwe ife tidasuntha kupita mbali ina mkatiakati mwa nkhondo, ndipo kenako tidabwerera kwa iye. Ndidamuona iye adakali ndi Mtumiki (Swallallaahu ‘alaihi wasallam) kudzipanga kukhala chichango cha Mtumiki swallallahu alaihi wasallam kumuteteza kwa adani).

Bibi Aaishah (Radhwiya Allaahu ‘anha) adati:

“Nthawi zonse Abu Bakr (Radhwiyallaahu ‘anhu) akamayankhula za tsiku la Uhud ankati:

“Tsiku limenelo linali la Talhah kwathunthu. Ine ndidali munthu oyamba kufika kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) chithereni nkhondo. Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa ine ndi Abu Ubaidah bun Jarrah: “Musamalire m’bale wako; (kutanthauza Talha).” Titamuyang’ana, tidapeza kuti adali ndi mabala opitirira makumi asanu ndi awiri pathupi pake. Olasidwa, kumenyedwa, komanso china mwa zala zake chidaduka. nthawi yomweyo tidamusamalira mwachangu mabala onse.””

Check Also

Mlamu wa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam)

Olemekezeka Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) adakwatira akazi okwana anayi. Aliyense mwa akazi ake anayi anali pachibale …