Nthawi ina Rasulullah (Swalla-Allaahu ‘alayhi wasallam) adamufunsa Busrah bint Safwan (Radhwiya-Allahu ‘anha) kuti ndi ndani amene ankafuna kukwatira mphwake, Umm Kulthuom bint Uqbah.
Adamufotokozera mayina a anthu ochepa omwe adamfunsira mphwakeyo, ndipo adamuwuzanso kuti mwa anthu omwe adamfunsira mphwakeyo ndi Abdur Rahman bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu).
Zitatero, Mtumiki (Swalla-Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa iye: “Muperere (m’bale wako Ummu Kulthoom) kwa Abdur Rahmaan bin Awf, ndithu, iye ndi mmodzi mwa Asilamu opambana. iyeyonso ali m’gulu la Asilamu abwino kwambiri”. (Al-Mu’jamul Awsat #1187)
M’nkhani ina, kwatchuridwanso kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adatinso: “Mutengere (m’bale wako Ummu Kulthoom) kwa mtsogoleri wa Asilamu, Abdur Rahman bin Awf. (Al-Isabah 14/502)
M’nkhani ina, kwanenedwanso kuti Mtumiki (Swalla-Allaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Ngati atakwatiwa ndi (Abdur Rahmaan bin Awf), adzakhala okhutira ndi okondwa.
Ummu Kulthoom (Radhwiya-Allaahu ‘anha) atamva izi, nthawi yomweyo adatumiza uthenga kwa mchimwene wake Uthmaan (Radhwiya Allahu ‘anhu) ndi kwa amalume ake, Khaalid bin Sa’eed (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti avomereze pempho la Abdur Rahmaan bin Awf (Radhwiya-Allaahu ‘anhu) ndi kukwatirana naye.
Pambuyo pa Nikaah, atayamba kukhalira limodzi, Ummu Kulthuom (Radhwiyallahu ‘anha) adati: “Wallah, ndasangalala kwambiri (ndi mwamuna wanga Abdur Rahmaan bin Awf).
Potero, mawu odalitsika a Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adakhaladi zenizeni.