Kulandira Uthenga Wabwino Wamwayi Ndi Chikhululukiro M’maloto

Usiku wina, Hazrat Abdur Rahmaan bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) adakomoka kwa nthawi yayitali chifukwa chakudwala kwake mpaka omwe anali pafupi naye adaganiza kuti mzimu wake wachoka. Anamuphimba ndi nsalu n’kuchokapo. Mkazi wake, Ummu Kulthum bint ‘Uqbah, nthawi yomweyo adapempha thandizo kwa Allah Ta’ala podekha ndi kuswali (monga talamulidwa kutero mu Qur’aan Kareem).

Hazrat Abdur Rahman bun Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) adakhala chikomokere kwa nthawi yayitali. Kenako, anatsitsimuka ndipo chinthu choyamba chimene analankhula chinali takbeer. Nawonso anthu omwe adali m’nyumbamo ndi amene anali pafupi nawo anakuwa. Kenako anawafunsa kuti, “Kodi ndinakomoka? Adayankha motsimikiza.

Kenako adati kwa iwo: “Mwanena zoona (Ndiri chikomokere) adanditenga angelo awiri amaonekedwe aanthu, ooneka ngati ovuta ndi okhwimitsa zinthu (m’maonekedwe awo). Iwo adati kwa ine, Pita kutsogolo, ife tikukutengera iwe kuchiweruzo kwa (Allah Ta’ala) Yemwe ndi Mwini mphamvu zoposa, Opereka chitetezo ndi Mtetezi wa chilichonse.

Kenako, ananditenga n’kupitiriza ulendo mpaka anakumana ndi mngelo owoneka ngati munthu amene anawafunsa kumene ankanditengera. (Iwo) adati: “Ife tikumutenga kuti akaweluzidwe kwa (Allah Ta’ala) yemwe ndi Wamphamvu zoposa, Amene amateteza ndi Wodziwa chilichonse.

Mngeloyo adawauza kuti: “Mubwezeretseni padziko lapansi, pakuti iye ndi mmodzi mwa anthu amene Allah Ta’ala wawalembera zabwino ndi chikhululuko iwo adakali m’mimba mwa amayi awo. Kuonjezera apo, Allah Taala wamuloreza kukhalabe padziko lapansi kwa nthawi ina kuti ana ake asangalare ndi kupindura ndi kukhala naye mpaka nthawi imene Allah Taala adzafune kumuchotsa padziko lapansi.

Zitachitika izi. Hazrat Abdur Rahmaan bun Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) adakhala ndi moyo kwa mwezi umodzi. Patadutsa mwezi umodzi, adamwalira malinga ndi lamulo la Allah Taala. (Dalaa ilun Nubuwwah 7/43, Taareekh Ibn ‘Asaakir 35/297)

Check Also

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu …