M’mahadithi olemekezeka, Olekezeka Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adatsimikizira ummah za Maonekedwe a Dajjaal a umunthu. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) kufotokoza za Dajjaal m’maonekedwe a munthu zikuonetsa kuti Dajjaal ndi munthu. Pa chifukwa chimenechi, chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah ndi chakuti Dajjaal ndi munthu, ndipo adzabwera pa dziko lapansi nthawi yoikika kuyandikira kwa Qiyaamah ngati chizindikiro chachikulu cha Qiyaamah ku ummah.
M’musimu muli maonekedwe 10 a Dajjaal omwe amatchuridwa mmahadith:
Chinthu Choyamba: Dajjaal kukhala Ndi Tsitsi Lokhala ngati lopotana
Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Usiku wina, ndidalota ndiri pa Ka’bah. Ndinapeza munthu wachilendo, amene anali ochititsa chidwi ndikukongora kwake, ndi khungu la mtundu osiyana. Tsitsi lake linali pakati pa mapirikaniro ake ndi mapewa ake atalipesa likutuluka madzi. Adagwira m’mapewa mwa anthu awiri ndipo akuchita tawaaf pa Ka’bah. Ndinafunsa kuti, ‘Ndi ndani uyu?’ Iwo anandiuza kuti, ‘Uyu ndi Maseeh bin Maryam (‘alaihis salaam).’ Kenako, ndinawona munthu wina wamfupi komanso ali ndi tsitsi lopiringizana kwambiri. Diso lake lakumanja lidali ndi vuto, ngati gilepu othudzuka. Ndinafunsa kuti, ‘Ndi ndani uyu?’ Iwo anandiuza kuti, ‘Uyu ndi Maseeh Dajjaal.’” (Saheeh Muslim #169)
Maonejedwe achiwiri: Dajjaal Ali Ndi Maso Olumala
Maso onse a Dajjaal adzakhala ndi vuto. Koma, diso limodzi lidzakhala lotsekeka ndi khungu, pamene linalo lidzafanana ndi gilepu othudzuka (monga momwe yafotokozera Hadith).
Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Inde, ndikudziwa momwe Dajjaal aliri. Adzakhala ndi mitsinje iwiri imene idzamutsatire kulikonse. Umodzi mwa mitsinje udzakhala ndi madzi abwinobwino, pomwe wina uzidzaoneka ngati moto oyaka mwaukali. Ngati wina angadzapezeke pamenepo, adzapite ku mtsinje omwe adzauone ngati ndi moto ndikudziponya m’menemo. Adzaike mutu wake pansi ndi kumwa madzi ake, popeza madzi ake ndi okoma. Ndithu, diso la Djjaal ndi lotsekeka pamwamba pake pali khungu lokhuthalapakati pa maso ake polembedwa mawu oti “kaafir” omwe okhulupilira wina aliyense adzakwanitsa kuwerenga amatha kuwerenga kaya samatha ” (Saheeh Muslim #2934)
Maonekedwe achitatu: Dajjaal adzakhala wamfupi, Onenepa ndi wazitho kwambiri.
Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Ndithudi, Maseeh Dajjaal, ndi wamfupi, zidendeni zake ndizotalikirana ndipo mapazi ake kutsogolo ndiopotokera mkati. Tsitsi lake ndilopotana kwambiri, limodzi mwa maso ake ndilosaona ndipo linalo ndilotong´oka silotulukamo komanso silolowa mkati, ngati maonekedwe ake angadzakusokonezeni, Ndiye mudziwe kuti Mbuye wanu Allah alibe diso losawona. ” (Sunan Abu Dawood #4320)
Muhadith ina, Hazrat Tameem Daari (radhwiyallahu ‘anhu), adamufotokoza Dajjaal ponena kuti, “ Kenako, Mwadzidzidzi, ali momwemo (muchigwa cha Wansembe) mudali munthu wamkulu kwambiri muchinyumba ndipo munthu ameneyo sitinamuonepo kalelonse.” (Saheeh Muslim #294)
Maonekedwe achinayi (4): Mapazi a Dajjaal adzakhala opotokera mkati (i.e. zidendene zake zidzakhala zotayana ndipo kutsogolo kwamapazi ake kudzakhala koyandikana)
Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Ndithudi, Maseeh Dajjaal, ndimunthu wamfupi, zindeneni zake ndi zotayana ndipo kutsogolo kwa mapazi ake ndiopotokera mkati.” (Sunan Abu Dawood #4320)
Maonekedwe achisanu (5): Dajjaal adzakhala ndi tsitsi lochuluka komanso lothothana.
Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Diso lakumanzere la Dajjaal ndilosaona ndipo tsitsi lake ndi lochuluka komanso lothothana. Ndipo azidzayenda ndi Jannah komanso Gehena. Gehena yake choonadi chake idzakhala Jannah ndipo Jannah yake choonadi chake idzakhala Gehena.” (Saheeh Muslim #2934)
Maonekedwe achisanu ndi chimodzimodzi (6): Dajjaal adzakhala ndi chipumi chotambasuka.
Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Choncho Maseeh Osocheretsayo, Ndi munthu amene chipumi chake ndi chotambasuka, Diso lake lakumanzere mlosaona ndipo gawo lapansi pakhosi pake ndi lalikulu. Ndipo. Ndipo ndichimodzimodzi ndi Abdul Uzza bin Qatan.” (Majma’uz Zawaa’id #12539)
Maonekedwe achisanu ndichiwiri: Dajjaal sadzakhala ndi ana.
Hadith yomwe ikupezeka mu swahihi Muslim ikulongosora kuti, “Kodi Rasulu- Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam) sananene kuti Dajjaal adzakhala osabereka komanso sadzakahala ndi ana?” (Saheeh Muslim #2927)
Maonekedwe achisanu ndi chitatu (8): Dajjaal ndi oyera khungu
Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adafunsidwa zokhuza Dajjaal ndipo anayankha nati, “Ndikuona kuti iye adzakhala okandapala ndiwazitho komanso oyera khungu. Diso lake limodzi ndi lotulukamo ngati nyenyezi yowala. Tsitsi lake ngati nthambi zamtengo.” (Musnad-e-Ahmed #3546)
Maonekedwe achisanu ndi chinayi (9): Mau oti “Kaafir” adzalembedwa pakati pamaso a Dajjaal
Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati mau oti , “ kaafir adzalembedwa pakati pamaso ake awiri, Munthu okhulupilila wina aliyense adzakwanitsa kuwerenga mawuwo kaya ndiodziwa kuwerenga ngakhale osadziwa kuwerenga” (Saheeh Muslim #2934)
Maonekedwe a khumi: Kufanana ndi kaafir, Abdul Uzza bin Qatan
Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati: “Ine ndikumufanizira (Dajjaal) ndi Abdul Uzza bin Qatan.” (Saheeh Muslim #2937)
Kuchokera m’mahadith omwe tatchulayi omwe ali afotokoza maonekedwe khumi a Dajjaal, tikumvetsa kuti Dajjaal ndi munthu. Akadakhala kuti Dajjaal ndi ziwanda, kapena osakanikirana pakati pa munthu ndi ziwanda, kapena dongosolo lapadziko lapansi, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) sakadamufotokoza mwa maonekedwe a umunthu wake.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu