Naufal bin lyaas al Huzali (rahimahullah) adati:
‘Tikakhala pamodzi ndi Abdur Rahman bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu), ndi kukhala naye chifupi kodabwitsa kusangalatsirenji. Tsiku lina, anatitengera kunyumba kwake kuti tikadye, Titakhala pansi kuti tidye ndipo mbale ya chakudya ya nyama ndi mkate inaperekedwa pamaso pathu, iye adayamba kulira.
Tidamufunsa: “Nchiyani chikukupangitsa kulira oh Abu Muhammad?” Adayankha: “Chomwe chandiliritsa ndikuti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adachoka pa dziko lapansi ndi moyo wakuti iye ndi banja lake sadadye mkate oti mpaka ndikukhuta (nthawi ya moyo wake). Ndikuopa kuti zisakhale kuti tikusungidwa m’mbuyo muno (padziko lapansi kuti tisangalare ndi zabwino izi) ndipo m’malo mwa izi, tidzakhala titalandidwa zabwino za tsiku lomaliza.” (Iswaabah 4/292)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu