Nkhondo ya Badr isanayambike, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) atamva kuti gulu la ochita malonda la Ma Quraish, lolemedwa ndi chuma chawo, lachoka ku Shaam (Syria) ndipo likubwerera ku Makkah Mukarramah, adatumiza Talhah bin Ubaidullah ndi Sa’iid radhwiyallahu anhuma kuti akasonkhanitse uthenga okhudza Gululi. Izi zidachitika masiku khumi Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) ndi Maswahabah asadanyamuke kuchoka ku Madinah Munawwarah kupita ku Badr.
Talhah ndi Saiid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhuma) adayenda mpaka kukafika pamalo otchedwa Hawraa. Adadikira pamenepo mpaka Gululo lidadutsa ndipo nthawi yomweyo adanyamuka ulendo opita ku Madinah Munawwarah kukamudziwitsa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). Komabe, asanakafike ku Madinah Munawwarah, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adali atauzidwa kale zambiri zokhudza Gululi ndipo adachoka ku Madinah Munawwarah pamodzi ndi gulu la ma Swahaabah kulitsatira gululo.
Asanachoke ku Madinah Munawwarah, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adawalimbikitsa Maswahaba kuti atsatire Gululo ndi kulimbana nalo. Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) Adati kwa iwo: “Mwina Allah Ta’ala akupatsani chuma chawocho munjira ya chofunkha.”
Olemekezeka Talhah ndi Said bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhuma) adafika ku Madina Munawwarah tsiku lomwe Asilamu adakumana ndi ma Kuffaar pankhondo ya Badr. Atauzidwa za nkhondoyi, nthawi yomweyo adanyamuka kupita ku Badr ndi cholinga chofuna kukathandizana ndi Asilamu kumenyana ndi makafiri. Komabe adakumana ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) panjira, pamalo otchedwa Turbaan, pomwe Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndi ma Swahaabah ankabwerako kuchokera ku Badr.
Ngakhale Talha bun Ubaidullah ndi Said bin Zaid (radhwiyallahu ‘anhuma) sadatenge nawo mbali pankhondoyi, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adawagawira gawo lina kuchokera ku zolandidwa pankhondoyo ndipo adawalonjeza kuti adzalandira mphotho yofanana ndi yomwe ma Swahaabah adachita nawo ku Badr.
M’zitabu zina, zikunenedwa kuti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) atawagawira gawo lina la chuma cholandidwa pankhondoyo, Said bin Zaid (Radhwiya Allahu ‘anhu) adamufunsa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) kuti: “Nanga bwanji za malipiro anga (ie, kodi nafenso tidzaikidwa m’gulu la malipiro a Badr)?” Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamutsimikizira kuti nawonso adzalandira malipiro ofanana ndi ma Swahaabah amene adatenga nawo gawo ku Badr.
Olemekezeka Sa’iid bun Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) adatengapo nawo gawo nkhondo zina zonse limodzi ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam).